Yesaya 5 BL92

Fanizo la munda wamphesa ndi kumasulira kwace

1 Ndiyimbire wokondedwa wanga nyimbo ya wokondedwa wanga ya munda wace wamphesa, Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa m'citunda ca zipatso zambiri;

2 ndipo iye anakumba mcerenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pace nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya.

3 Ndipo tsopano, inu okhala m'Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, weruzanitu mlandu wa ine ndi munda wanga wamphesa.

4 Ndikanacitanso ciani ndi munda wanga wamphesa, cimene sindinacite m'menemo; muja ndinayembekeza kuti udzabala mphesa, wabaliranji mphesa zosadya?

5 Ndipo tsopano ndidzakuuzani cimene nditi ndicite ndi munda wanga wamphesa; ndidzacotsapo chinga lace, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lace, ndipo zidzapondedwa pansi;

6 ndipo ndidzaupasula; sudzadzomboleredwa kapena kulimidwa; koma padzamera lunguzi ndi minga; ndidzalamuliranso mitambo kuti isabvumbwepo mvula.

7 Cifukwa kuti munda wamphesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israyeli, ndi anthu a Yuda, mtengo wace womkondweretsa; Iye anayembekeza ciweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza cilungamo, koma onani kupfuula.

8 Tsoka kwa iwo amene aphatikiza nyumba ndi nyumba, amene alumikiza munda ndi munda, kufikira padzapanda malo, ndipo inu mudzasiyidwa nokha pakati pa dziko!

9 M'makutu anga, ati Yehova wa makamu, Zoonadi nyumba zambiri zidzakhala bwinja, ngakhale zazikuru ndi zokoma zopanda wokhalamo.

10 Cifukwa kuti munda wamphesa wa madera khumi udzangobala mbiya imodzi, ndi mbeu za nsengwa khumi zidzangobala nsengwa imodzi.

11 Tsoka kwa iwo amene adzuka m'mamawa kuti atsate zakumwa zaukali; amene acezera usiku kufikira vinyo awaledzeretsal

12 Ndipo zeze ndi mgoli, ndi lingaka ndi citoliro, ndi vinyo, ziri m'mapwando ao; koma iwo sapenyetsa nchito ya Yehova; ngakhale kuyang'ana pa macitidwe a manja ace.

13 Cifukwa cace anthu anga amuka m'nsinga, cifukwa ca kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi.

14 Ndipo manda akuza cilakolako cace, natsegula kukamwa kwace kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo.

15 Munthu wonyozeka waweramitsidwa, ndi munthu wochuka watsitsidwa, ndi maso a wodzikweza atsitsidwa;

16 koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'ciweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'cilungamo.

17 Pamenepo ana a nkhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zacilendo zidzadyapo.

18 Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zacabe, ndi cimo ngati ndi cingwe ca gareta;

19 amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize nchito yace kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israyeli uyandikire, udze kuti tiudziwe!

20 Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!

21 Tsoka kwa iwo amene adziyesera anzeru ndi ocenjera!

22 Tsoka kwa iwo amene ali a mphamvu yakumwa vinyo, ndi anthu olimba akusanganiza zakumwa zaukali;

23 amene alungamitsa woipa pa cokometsera mlandu, nacotsera wolungama cilungamo cace!

24 Cifukwa cace monga ngati lilime la moto likutha ciputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wobvunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati pfumbi; cifukwa kuti iwo akana cilamulo ca Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israyeli.

25 Cifukwa cace mkwiyo wa Yehova wayaka pa anthu ace, ndipo Iye watambasulira iwo dzanja lace, nawakantha, ndipo zitunda zinanthunthumira, ndi mitembo yao inali ngati zinyatsi pakati pa makwalala. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.

26 Ndipo Iye adzakwezera a mitundu yakutari mbendera, nadzawayimbira mluzu, acokere ku malekezero a dziko; ndipo taonani, iwo adzadza ndi liwiro msanga msanga;

27 palibe amene adzalema, kapena adzapunthwa mwa iwo, palibe amene adzaodzera kapena kugona tulo; ngakhale lamba la m'cuuno mwao silidzamasuka, kapena comangira ca nsapato zao sicidzaduka;

28 amene mibvi yao ili yakuthwa, ndi mauta ao onse athifuka; ziboda za akavalo ao zidzayesedwa ngati mwala, ndi njinga zao ngati kabvumvulu;

29 kubangula kwao kudzafana ndi mkango, iwo adzabangula ngati ana a mikango, inde iwo adzabangula, nadzagwira nyama, naicotsa bwino opanda wakupulumutsa.

30 Ndipo iwo adzawabangulira tsiku limenelo ngati kukokoma kwa nyanja; ndipo wina ayang'ana padziko, taonani mdima ndi nsautso, kuyera kwadetsedwanso m'mitambo yace.