Yesaya 59 BL92

Aulula zoipa za mtundu wao

1 Taonani, mkono wa Yehova sufupika, kuti sungathe kupulumutsa; khutu lace siliri logontha, kuti silingamve;

2 koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo macimo anu abisa nkhope yace kwa inu, kuti Iye sakumva.

3 Pakuti manja anu adetsedwa ndi mwazi, ndi zala zanu ndi mphulupulu, milomo yanu yanena zonama, lilime lanu lilankhula moipa.

4 Palibe woturutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwacabe, nanena zonama; iwo atenga kusayeruzika ndi kubala mphulupulu,

5 Iwo afungatira mazira a mamba aswetse, naluka ukonde wa tandaude; iye amene adya mazira ace amafa, ndi coswanyikaco cisweka nicikhala songo.

6 Maukonde ao sadzakhala zobvala, sadzapfunda nchito zao; nchito zao ziri nchito zoipa, ndi ciwawa ciri m'manja mwao.

7 Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosacimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi cipasuko ziri m'njira mwao.

8 Njira ya mtendere saidziwa, ndipo palibe ciweruziro m'mayendedwe mwao; akhotetsa njira zao; ali yense ayenda m'menemo sadziwa mtendere.

9 Cifukwa cace ciweruziro ciri patari ndi ife, ndi cilungamo sicitipeza; tiyang'anira kuunika, koma taona mdima; tiyang'anira kuyera, koma tiyenda m'usiku.

10 Tiyambasira khoma ngati wakhungu, inde tiyambasa monga iwo opanda maso; tipunthwa usana monga m'cizirezire; tiri m'malo amdima ngati akufa.

11 Tonse tibangula ngati zirombo, ndi kulira maliro zolimba ngati nkhunda; tiyang'anira ciweruziro koma palibe; tiyang'anira cipulumutso koma ciri patari ndi ife.

12 Pakuti zolakwa zathu zacuruka pamaso pa Inu, ndipo macimo athu atineneza ife; pakuti zolakwa zathu ziri ndi ife, ndipo zoipa zathu tizidziwa;

13 ndizo kulakwabe ndi kukanabe Yehova, ndi kuleka kutsata Mulungu wathu, kulankhula zotsendereza ndi kupanduka, kuganizira ndi kunena pakamwa mau akunyenga oturuka mumtima.

14 Ndipo ciweruziro cabwerera m'mbuyo, ndi cilungamo caima patari; pakuti coona cagwa m'khwalala, ndi kuongoka sikungalowe.

15 Inde coona cisoweka; iye amene asiya coipa, zifunkhidwa zace; ndipo Yehova anaona ici, ndipo cidamuipira kuti palibe ciweruzo.

16 Ndipo Iye anaona kuti palibe munthu, nazizwa kuti palibe wopembedzera; cifukwa cace mkono wace wace unadzitengera yekha cipulumutso; ndi cilungamo cace cinamcirikiza.

17 Ndipo anabvala cilungamo monga cida ca pacifuwa, ndi cisoti ca cipulumutso pamutu pace; nabvala zobvala zakubwezera cilango, nabvekedwa ndi cangu monga copfunda,

18 Monga mwa nchito zao momwemo Iye adzabwezera amaliwongo ace ukali, nadzabwezera adani ace cilango; nadzabwezeranso zisumbu cilango.

19 Comweco iwo adzaopa dzina la Yehova kucokera kumadzulo, ndi ulemerero wace kumene kuturukira dzuwa; pakuti pamene mdani adzafika ngati cigumula, mzimu wa Yehova udzamkwezera mbendera yomletsa.

20 Ndipo Mombolo adzafika ku Ziyoni, ndi kwa iwo amene atembenuka kusiya kulakwa mwa Yakobo, ati Yehova.

21 Ndipo kunena za. Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzacoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi ku nthawi zonse.