Yesaya 13 BL92

Aneneratu za kutyoka kwa ufumu wa Babulo, ndi kubweza Israyeli kwao

1 Katundu wa Babulo, imene anaiona Yesaya mwana wa Amozi.

2 Kwezani mbendera pa phiri loti se, kwezani mau kwa iwo, kodolani kuti alowe m'zipata za akuru.

3 Ine ndalamulira opatulidwa anga, inde, ndaitana amphamvu anga, acite mkwiyo wanga, okondwerera ndi ukuru wanga.

4 Mau a khamu m'mapiri, akunga amtundu waukuru wa anthu, mau a phokoso la maufumu a mitundu yosonkhanidwa! Yehova wa makamu asonkhanitsa khamu kunkhondo.

5 Acokera m'dziko lakutari, ku malekezero a thambo, ngakhale Yehova, ndi zida za mkwiyo wace, kuti aononge dziko lonse.

6 Kuwani inu; pakuti tsiku la Yehova liri pafupi; lidzafika monga cionongeko cocokera kwa Wamphamvuyonse.

7 Cifukwa cace manja onse adzafoka, ndi mitima yonse ya anthu idzasungunuka;

8 ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.

9 Taonani tsiku la Yehova lidza, lankhanza, ndi mkwiyo ndi kukalipira kwaukali; kupasula dziko, ndi kudzaonongamo akucimwa psiti.

10 Cifukwa nyenyezi za kumwamba ndi makamu ao sizidzawala; dzuwa lidzada m'kuturuka kwace, ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwace.

11 Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, cifukwa ca kuipa kwao, ndi oipa cifukwa ca mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsya.

12 Ndipo ndidzacepsa anthu koposa golidi, ngakhale anthu koposa golidi weniweni wa ku Ofiri.

13 Cifukwa cace ndidzanthunthumiritsa miyamba, ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka kucokera m'malo ace, m'mkwiyo wa Yehova wa makamu, tsiku la mkwiyo wace waukali.

14 Ndipo padzakhala kuti monga mbawala yothamangitsidwa, ndi monga nkhosa zosazisonkhanitsa anthu, adzatembenukira yense kwa anthu ace, nathawira yense ku dziko lace.

15 Onse opezedwa adzapyozedwa, ndi onse ogwidwa adzagwa ndi lupanga.

16 Makanda ao adzatswanyidwe pamaso pao; m'nyumba mwao mudzafunkhidwa, ndi akazi ao adzakakamizidwa.

17 Taonani, ndidzawautsira Amedi, amene sadzasamalira siliva, ngakhale golidi sadzakondwera naye.

18 Mauta ao adzatha anyamata; ndipo sadzacitira cisoni cipatso ca mimba; diso lao silidzaleka ana.

19 Ndipo Babulo, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Akasidi anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.

20 Anthu sadzakhalamo konse, sadzakhalamo mbadwo ndi mbadwo; M-arabu sadzamanga hema wace pamenepo; abusa sadzagonetsa makamu ao kumeneko.

21 Koma zirombo za m'cipululu zidzagona pamenepo; nyumba zao zidzadzala ndi zakukuwa; ndipo nthiwatiwa zidzakhala pamenepo, ndipo atonde adzajidimuka pamenepo,

22 Ndipo mimbulu idzalira m'maboma ao, ndi ankhandwe m'manyumba ao abwino; ndi nthawi yace iyandikira, ndi masiku ace sadzacuruka.