Yesaya 32 BL92

Ufumu wa mfumu yolungama

1 Taonani mfumu idzalamulira m'cilungamo, ndi akalonga adzalamulira m'ciweruzo.

2 Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira cimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikuru m'dziko lotopetsa.

3 Ndipo maso a iwo amene aona sadzatsinzina, ndi makutu a iwo amene amva adzamvera.

4 Mtimanso wansontho udzadziwa nzeru, ndi lilume la acibwibwi lidzalankhula zomveka msanga.

5 Wopusa sadzayesedwanso woolowa manja, ngakhale wouma manja sadzayesedwa mfulu.

6 Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wace udzacita mphulupulu, kucita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa cakumwa ca waludzu.

7 Zipangizonso za womana ziri zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.

8 Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.

Cilangizo ca kwa akazi

9 Ukani, akazi inu, amene mulinkukhala phe, mumve mau anga; mu ana akazi osasamalira, cherani makutu pa kulankhula kwanga.

10 Pakutha caka, kudza masiku ena inu mudzabvutidwa, inu akazi osasamalira; pakuti masika a mphesa adzasoweka, sadzatuta konse.

11 Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhalaphe; bvutidwani, inu osasamalira, bvulani mukhale marisece, nimumange ciguduli m'cuuno mwanu.

12 Iwo adzadzimenya pazifuwa cifukwa ca minda yabwino, cifukwa ca mpesa wobalitsa.

13 Pa dziko la anthu anga padzafika minga ndi lunguzi; inde pa nyumba zonse zokondwa, m'mudzi wokondwerera;

14 pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mudzi wa anthu ambiri udzakhala bwinja; citunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba ku nthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;

15 kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kucokera kumwamba, ndi cipululu cidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.

16 Pamenepo ciweruzo cidzakhala m'cipululu, ndi cilungamo cidzakhala m'munda wobalitsa.

17 Ndi nchito ya cilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata cilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika ku nthawi zonse.

18 Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.

19 Koma kudzagwa matalala m'kugwa kwace kwa nkhalango; ndipo mudzi udzagwetsedwa ndithu.

20 Odala muli inu, amene mubzala m'mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng'ombe ndi buru.