Yesaya 41 BL92

Yehova yekha ndiye Mulungu, lsrayeli amkhulupirire Iye yekha yekha

1 Khalani cete pamaso pa Ine, zisumbu inu, anthu atengenso mphamvu; ayandikire; pamenepo alankhule; tiyeni, tiyandikire pamodzi kuciweruziro.

2 Ndani anautsa wina wocokera kum'mawa, amene amuitana m'cilungamo, afike pa phazi lace? Iye apereka amitundu patsogolo pace, namlamuliritsa mafumu; nawapereka monga pfumbi ku lupanga lace, monga ciputu couluzidwa ku uta wace.

3 Iye awathamangitsa, napitirira mwamtendere; pa njira imene asanapitemo ndi mapazi ace.

4 Ndani wacipanga, nacimariza ico, kuchula mibadwo ciyambire? Ine Yehova, ndine woyamba, ndi pacimariziro ndine ndemwe.

5 Zisumbu zinaona niziopa; malekezero a dziko lapansi ananthunthumira; anayandikira, nafika.

6 Iwo anathangata yense mnansi wace, ndi yense anati kwa mbale wace, Khala wolimba mtima.

7 Cotero mmisiri wa mitengo analimbikitsa wosula golidi, ndi iye amene asalaza ndi nyundo anamlimbikitsa iye amene amenya posulira, nanena za kulumikiza ndi nthobvu, Kuti kwabwino; ndipo iye akhomera fanolo misomali kuti lisasunthike.

8 Koma iwe, Israyeli, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa;

9 iwe amene ndinakuwira iwe zolimba kucokera ku malekezero a dziko lapansi, ndi kukuitana iwe kucokera m'ngondya zace, ndipo ndinati kwa iwe, Ndiwe mtumiki wanga ndakusankha, sindinakutaya kunja;

10 usaope, pakuti Ine ndiri pamodzi ndi iwe; usaopsyedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakucirikiza ndi dzanja langa lamanja la cilungamo.

11 Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati cabe, nadzaonongeka.

12 Iwe udzawafuna osawapeza, ngakhale iwo amene akangana ndi iwe; ocita nkhondo ndi iwe, adzakhala ngati cabe, ndi monga kanthu kopanda pace.

13 Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.

14 Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israyeli; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israyeli.

15 Taona, ndidzakuyesa iwe coombera tirigu catsopano cakuthwa cokhala ndi mano; iwe udzaomba mapiri ndi kuwapera asalale, ndi kusandutsa zitunda mungu.

16 Iwe udzawakupa, ndi mphepo idzawauluza; ndipo kabvumvulu adzawamwaza; ndipo iwe udzasangalala mwa Yehova, udzadzikuza mwa Woyera wa Israyeli,

17 Wosauka ndi wosowa afuna madzi, ndipo palibe, ndi lilume lao lilephera, cifukwa ca ludzu; Ine Yehova ndidzawayankha, Ine Mulungu wa Israyeli sindidzawasiya.

18 Ndidzagwetsa mitsinje pazitunda zoti se, ndi akasupe pakati pa zigwa; ndidzasandutsa cipululu, cikhale thamanda lamadzi, ndi mtunda wouma ukhale magwero a madzi.

19 Ndidzabzala m'cipululu mkungudza, ndi msangu, ndi mcisu, ndi mtengo waazitona; ndidzaika m'cipululu pamodzi mlombwa, ndi mkuyu, ndi naphini;

20 kuti iwo aone ndi kudziwa, ndi kulingalira, ndi kumvetsa pamodzi, kuti dzanja la Yehova lacita ici, ndipo Woyera wa Israyeli wacilenga ici.

21 Onetsani mlandu wanu, ati Yehova; turutsani zifukwa zanu zolimba, ati Mfumu ya Yakobo.

22 Aziturutse, atichulire ife, cimene cidzaoneka; chulani inu zinthu zakale, zinali zotani, kuti ife tiganizire pamenepo, ndi kudziwa mamariziro ao; kapena tionetseni ife zinthu zimene zirinkudza.

23 Chulani zinthu zimene zirinkudza m'tsogolo, kuti ife tidziwe kuti inu ndinu milungu; inde, citani zabwino, kapena citani zoipa, kuti ife tiopsyedwe, ndi kuona pamodzi.

24 Taonani, inu muli acabe, ndi nchito yanu yacabe; wonyansa ali iye amene asankha inu.

25 Ndautsa wina wakucokera kumpoto; ndipo iye wafika wakucokera poturuka dzuwa, amene achula dzina langa; ndipo iye adzafika pa olamulira, monga matope, ndi monga muumbi aponda dothi la mbiya.

26 Ndani wachula ico ciyambire, kuti ife ticidziwe? ndi nthawi zakale, kuti ife tinene, Iye ali wolungama? inde, palibe wina amene achula, inde, palibe wina amene asonyeza, inde, palibe wina amene amvetsa mau anu.

27 Poyamba Ine ndidzati kwa Ziyoni, Taona, taona iwo; ndipo ndidzapereka kwa Yerusalemu wina, amene adza ndi mau abwino.

28 Ndipo pamene ndayang'ana, palibe munthu; ngakhale mwa iwo, palibe phungu, amene angathe kuyankha mau, pamene ndiwafunsa.

29 Taona, iwo onse, nchito zao zikhala zopanda pace ndi zacabe; mafano ao osungunula ndiwo mphepo ndi masokonezo.