Yesaya 45 BL92

Yehova amuyesa Koresi cipangizo cace

1 Atero Yehova kwa wodzozedwa wace kwa Koresi, amene dzanja lace lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pace, ndipo ndidzamasula m'cuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pace, ndi zipata sizidzatsekedwa:

2 Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzatyolatyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapici acitsulo;

3 ndipo ndidzakupatsa iwe cuma ca mumdima, ndi zolemera zobisika za m'malo am'tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israyeli.

4 Ndakuitana iwe dzina lako, cifukwa ca Yakobo mtumiki wanga ndi Israyeli wosankhidwa wanga; ndakuonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziwa Ine.

5 Ine ndiri Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'cuuno, ngakhale sunandidziwa;

6 kuti anthu akadziwe kucokera ku maturukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso.

7 Ine ndilenga kuyera ndi mdima, Ine ndilenga mtendere ndi coipa, Ine ndine Yehova wocita zinthu zonse zimenezi.

8 Igwani pansi, inu m'mwamba, kucokera kumwamba, thambo litsanulire pansi cilungamo; dziko lapansi litseguke, kuti libalitse cipulumutso, nilimeretse cilungamo cimere pamodzi; Ine Yehova ndinacilenga cimeneco.

9 Tsoka kwa iye amene akangana ndi Mlengi wace! phale mwa mapale a dziko lapansi! Kodi dongo linganene kwa iye amene aliumba, Kodi upanga ciani? pena nchito yako, Iye alibe manja?

10 Tsoka kwa iye amene ati kwa atate wace, Kodi iwe ubalanji? pena kwa mkazi, Ulikusauka ninji iwe?

11 Atero Yehova Woyera wa Israyeli ndi Mlengi wace, Ndifunse Ine za zinthu zimene zirinkudza; za ana anga amuna, ndi za nchito ya manja anga, ndilamulireni Ine.

12 Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyulula kumwamba, ndi zonse za m'menemo, ndinazilamulira ndine.

13 Ine ndautsa Koresi m'cilungamo, ndipo ndidzalungamitsa njira zace zonse; iye adzamanga mudzi wanga, nadzaleka andende anga anke mwa ufulu, wosati ndi mtengo pena mphotho, ati Yehova wa makamu.

14 Atero Yehova, Nchito ya Aigupto, ndi malonda a Kusi, ndi a Sabea, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m'maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.

15 Ndithu Inu ndinu Mulungu, amene mudzibisa nokha, Mulungu wa Israyeli, Mpulumutsi.

16 Iwo adzakhala ndi manyazi, inde, adzathedwa nzeru onsewo; adzalowa m'masokonezo pamodzi, amene apanga mafano.

17 Koma Israyeli adzapulumutsidwa ndi Yehova ndi cipulumutso cosatha; inu simudzakhala ndi manyazi, pena kuthedwa nzeru ku nthawi zosatha.

18 Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwacabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.

19 Ine sindinanena m'tseri m'malo a dziko la mdima; Ine sindinati kwa mbeu ya Yakobo, Mundifune Ine mwacabe; Ine Yehova ndinena cilungamo, ndinena zimene ziri zoona.

20 Sonkhanani nokha, mudze; yandikirani cifupi pamodzi, inu amene mwapulumuka amitundu; iwo alibe nzeru, amene anyamula mtengo wa fano lao losema, ndi kupemphera mlungu wosakhoza kupulumutsa.

21 Nenani inu, turutsani mlandu wanu; inde, acite uphungu pamodzi; ndani waonetsa ici ciyambire nthawi yakale? ndani wanena ici kale? kodi si ndine Yehova? ndipo palibenso Mulungu wina popanda Ine; Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi; palibenso wina popanda Ine.

22 Yang'anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina.

23 Ndadzilumbira ndekha, mau acokera m'kamwa mwanga m'cilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.

24 Koma mwa Yehova yekha, wina adzati kwa Ine, muli cilungamo ndi mphamvu; ngakhale kwa Iyeyo anthu adzafika, ndi onse amene anamkwiyira, adzakhala ndi manyazi.

25 Mwa Yehova mbeu yonse ya Israyeli idzalungamitsidwa ndi 7 kudzikuza.