1 Tsoka okhulupirira Aigupto. Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere cimo ndi cimo;
2 amene ayenda kutsikira ku Aigupto, osafunsa kukamwa kwanga, kudzilimbitsa iwo okha ndi li mphamvu za Farao, ndi kukhulupirira mthunzi wa Aigupto
3 Cifukwa cace mphamvu za Farao zidzakhala kwa inu manyazi, ndi kukhulupirira mthunzi wa Aigupto kudzakhala cisokonezo canu.
4 Pakuti akalonga ace ali pa Zaani, ndi mithenga yace yafika ku Hanesi.
5 Iwo onse adzakhala ndi manyazi, ndi anthu amene sangapindule nao kanthu, amene sakhala kwa iwo thangata, pena phindu, koma manyazi ndi citonzo.
6 Katundu wa zirombo za kumwera.M'dziko lobvuta ndi lopweteka, kumeneko kucokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula cuma cao pamsana pa aburu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamila, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.
7 Pakuti thangata la Aigupto liri lacabe, lopanda pace; cifukwa cace ndamucha wonyada, wokhala cabe.
8 Tsopano pita, ukalembe mauwa pamaso pao pathabwa, nuwalembe m'buku, kuti akakhalebe ku nthawi yam'tsogolo, mboni ya masiku onse.
9 Pakuti ali anthu opanduka, ana onama, ana osafuna kumva cilamulo ca Yehova;
10 amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;
11 cokani inu munjira, patukani m'bande, tiletsereni Woyera wa Israyeli pamaso pathu.
12 Cifukwa cace atero Woyera wa Israyeli, Popeza inu mwanyoza mau awa, nimukhulupirira nsautso ndi mphulupulu, ndi kukhala m'menemo;
13 cifukwa cace kuipa kumeneku kudzakhala kwa inu monga pogumuka pofuna kugwa, monga potukuka m'khoma lalitari, kugumuka kwace kufika modzidzimutsa dzidzidzi.
14 Ndipo Iye adzagumulapo, monga mbiya ya woumba isweka, ndi kuiswaiswa osaileka; ndipo sipadzapezedwa m'zigamphu zace phale lopalira moto pacoso, ngakhale lotungira madzi padziwe.
15 Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israyeli, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala cete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafuna.
16 Koma munati, Iai, pakuti tidzathawa pa akavalo; cifukwa cace inu mudzathawadi; ndipo ife tidzakwera pa akavalo aliwiro; cifukwa cace iwo amene akuthamangitsani, adzakhala aliwiro.
17 Cikwi cimodzi cidzathawa pakuwadzudzula mmodzi; pakukudzudzulani anthu asanu mudzathawa; kufikira inu mudzasiyidwa ngati mlongoti pamwamba pa phiri, ndi ngati mbendera pamwamba pa citundu.
18 Cifukwa cace Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo cifukwa cace Iye adzakuzidwa, kuti akucitireni inu cifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa ciweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.
19 Pakuti anthu adzakhala m'Ziyoni pa Yerusalemu; iwe sudzaliranso, Iye ndithu adzakukomera mtima pakumveka kupfuula kwako; pakumva Iye adzayankha.
20 Ndipo ngakhale Ambuye adzakupatsani inu cakudya ca nsautso, ndi madzi a cipsinjo, koma aphunzitsi ako sadzabisikanso, koma maso ako adzaona aphunzitsi ako;
21 ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.
22 Ndipo mudzaipitsa cokuta ca mafano ako, osema asiliva, ndi comata ca mafano ako osungunula agolidi; udzawataya ngati kanthu konyansa, udzati kwa iwo, Cokani.
23 Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wace adzaca bwino ndi kucuruka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo akuru.
24 Momwemonso ng'ombe ndi ana a buru olima nthaka adzadya cakudya cocezera, cimene capetedwa ndi cokokolera ndi mkupizo.
25 Ndipo pamwamba pa mapiri akuru onse, ndipa zitunda zonse zazitaritari padzakhala mitsinje ndi micerenje ya madzi, tsiku lophana lalikuru, pamene nsanja zidzagwa.
26 Komanso kuwala kwace kwa mwezi kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa, ndi kuwala kwa dzuwa kudzakula monga madzuwa asanu ndi awiri, monga kuwala kwa masiku asanu ndi awiri, tsiku limenelo Yehova adzamanga bala la anthu ace, nadzapoletsa khana limene anawakantha ena.
27 Taonani, dzina la Yehova licokera kutari, mkwiyo wace uyaka, malawi ace ndi akuru; milomo yace iri yodzala ndi ukali, ndi lilime lace liri ngati moto wonyambita;
28 ndi mpweya wace uli ngati mtsinje wosefukira, umene ufikira m'khosi, kupeta mitundu ya anthu ndi copetera ca cionongeko; ndi capakamwa calakwitsa, cidzakhala m'nsagwada za anthu.
29 Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi citoliro, kufikira ku phiri la Yehova, ku thanthwe la Israyeli,
30 Ndipo Yehova adzamveketsa mau ace a ulemerero, ndipo adzaonetsa kumenya kwa dzanja lace, ndi mkwiyo wace waukali, ndi lawi la moto wonyambita, ndi kuomba kwa mphepo, ndi mkuntho ndi matalala.
31 Pakuti ndi mau a Yehova Asuri adzatyokatyoka, ndi ndodo yace adzammenya.
32 Ndipo nthawi zonse Yehova adze vakantha ndi ndodo yosankhikayo, padzamveka mangaka ndi zeze; ndi m'nkhondo zothunyana-thunyana, Iye adzamenyana nao.
33 Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde cifukwa ca mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wacewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wasulfure.