Yesaya 43 BL92

Mulungu Yehova yekha apulumutsa Israyeli

1 Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israyeli, Usaope, cifukwa ndakuombola iwe, ndakuchula dzina lako, iwe uli wanga.

2 Pamene udulitsa pamadzi ndiri pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsya; ngakhale lawi silidzakutentha.

3 Cifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israyeli, Mpulumutsi wako; ndapatsa Aigupto dombolo lako, Etiopia ndi Seba m'malo mwako.

4 Pokhala iwe wa mtengo wapatari pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako.

5 Usaope; pakuti Ine ndiri ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kucokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kucokera kumadzulo.

6 Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga amuna kucokera kutari, ndi ana anga akazi kucokera ku malekezero a dziko lapansi;

7 yense wochedwa dzina langa, amene ndinamlenga cifukwa ca ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.

8 Turutsani anthu akhungu, amene ali ndi maso, ndi agonthi, amene ali ndi makutu.

9 Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ici ndi kuonetsa ife zinthu zakale? atenge mboni zao, kuti abvomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi.

10 Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina.

11 Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha.

12 Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wacilendo pakati pa inu; cifukwa cace inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.

13 Inde ciyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira nchito, ndipo ndani adzaletsa?

14 Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israyeli: Cifukwa ca inu ndatumiza ku Babulo, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Akasidi m'ngalawa za kukondwa kwao.

15 Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israyeli, Mfumu yanu,

16 Atero Yehova, amene akonza njira panyanja, ndi popita m'madzi amphamvu;

17 amene aturutsa gareta ndi ka valo, nkhondo ndi mphamvu; iwo agona pansi pamodzi sadzaukai; iwo atha, azimidwa ngati lawi.

18 Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale.

19 Taonani, ine ndidzacita cinthu catsopano; tsopano cidzaoneka; kodi simudzacidziwa? Ndidzakonzadi njira m'cipululu, ndi mitsinje m'zidalala.

20 Nyama za m'thengo zidzandilemekeza, ankhandwe ndi nthiwatiwa; cifukwa ndipatsa madzi m'cipululu, ndi mitsinje m'mkhwangwala, ndimwetse anthu anga osankhika;

21 anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.

22 Komabe iwe sunandiitane Ine, Yakobo; koma iwe walema ndi Ine, Israyeli.

23 Iwe sunanditengere Ine zoweta zazing'ono za nsembe zopsereza zako; kapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Sindinakutumikiritsa ndi nsembe zaufa, kapena kukutopetsa ndi zonunkhira.

24 Iwe sunandigulire Ine nzimbe ndi ndarama, pena kundikhutitsa ndi mafuta a nsembe zako. Koma iwe wanditumikiritsa ndi macimo ako, wanditopetsa ndi mphulupulu zako.

25 Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, cifukwa ca Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira macimo ako.

26 Undikumbutse Ine; tiyeni, tinenane pamodzi; fotokoza mlandu wako, kuti ukalungamitsidwe.

27 Atate wako woyamba anacimwa, ndi otanthauzira ako andilakwira Ine.

28 Cifukwa cace ndidzaipitsa akuru a kacisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israyeli akhale citonzo.