Yesaya 64 BL92

1 Mwenzi mutang'amba kumwamba ndi kutsikira pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu;

2 monga pamene moto uyatsa zitsamba, ndi moto uwiritsa madzi; kudziwitsa kwa amaliwongo anu dzina lanu, kuti amitundu anthunthumire pamaso panu,

3 Pamene Inu munacita zinthu zoopsya, zimene ife sitinayang'anira, Inu munatsika, mapiri anagwedezeka pamaso panu.

4 Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira nchito iye amene amlindirira Iye.

5 Inu mukomana ndi iye amene akondwerera, nacita cilungamo, iwo amene akumbukira Inu m'njira zanu; taonani Inu munakwiya, ndipo ife tinacimwa; takhala momwemo nthawi yambiri, kodi tidzapulumutsidwa?

6 Pakuti ife tonse takhala ngati wina amene ali wosakonzeka; ndi zolungama zathu zonse ziri ngati cobvala codetsedwa; ndipo ife tonse tifota monga tsamba, ndi zoipa zathu zitiuluza monga mphepo.

7 Ndipo palibe amene aitana dzina lanu, amene adzikangamiza yekha kugwiritsa Inu; pakuti Inu mwatibisira nkhope yanu, ndipo mwatinyeketsa ndi zoipa zathu.

8 Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tiri dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tiri nchito ya dzanja lanu.

9 Musakwiye kopambana, Yehova, musakumbukire zoipa nthawi zonse; taonani, yang'anani ife, tikupembedzani Inu, ife tonse tiri anthu anu.

10 Midzi yanu yopatulika yasanduka cipululu, Ziyoni wasanduka cipululu, Yerusalemu wasanduka bwinja.

11 Nyumba yathu yopatulika ndi yokongola, m'mene makolo athu anakutamandani Inu, yatenthedwa ndi moto; ndi zinthu zathu zonse zokondweretsa zapasuka.

12 Kodi mudzadziletsa pa zinthuzi, Yehova? Kodi Inu mudzakhala cete ndi kutibvutitsa ife zolimba?