1 Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efraimu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wace wokongola, limene liri pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'cigwa ca nthaka yabwino.
2 Taonani, Ambuye ali ndi wina wamphamvu wolimba; ngati cimphepo ca matalala, mkuntho wakuononga, ngati namondwe wa madzi amphamvu osefukira, adzagwetsa pansi ndi dzanja lamphamvu.
3 Korona wakunyada wa oledzera a Efraimu adzaponderezedwa;
4 ndi duwa lakufota la ulemerero wace wokongola, limene liri pamutu pa cigwa ca nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kuca malimwe asanafike; polona wakupenya imeneyo, amaidya iri m'dzanja lace.
5 Tsiku limenelo Yehova wa makamu adzakhala korona wa ulemerero, ndi korona wokongola kwa anthu ace otsala:
6 ndipo adzakhala mzimu wa ciweruziro kwa oweruza mirandu, ndi mphamvu kwa iwo amene abweza nkhondo pacipata.
7 Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasocera ndi cakumwa caukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi cakumwa caukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasocera ndi cakumwa caukali, adzandima popenya, napunthwa poweruza.
8 Pakuti magome onse adzazidwa ndi masanzi ndi udio, palibe malo okonzeka.
9 Kodi Mulungu adzaphunzitsa yani nzeru? Kodi Iye adzamvetsa yani uthengawo? iwo amene aletsedwa kuyamwa, nacotsedwa pamabere?
10 Pakuti pali langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono.
11 Iai, koma ndi anthu a milomo yacilendo, ndi a lilume lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa;
12 amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva.
13 Cifukwa cace mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa cambuyo, ndi kutyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.
14 Cifukwa cace imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a m'Yerusalemu.
15 Cifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tabvomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;
16 cifukwa cace Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika m'Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangondya, wa mtengo wace wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.
17 Ndipo ndidzayesa ciweruziro cingwe coongolera, ndi cilungamo cingwe colungamitsira ciriri; ndipo matalala adzacotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.
18 Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kubvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalepereka; popita mliri woopsya udzakuponderezani pansi.
19 Nthawi zonse umapita, udzakutengani; cifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsya kokha, kumva mbiri yace.
20 Pakuti kama wafupika, munthu sangatambalale pamenepo; ndi copfunda cacepa, sicingamfikire.
21 Pakuti Yehova adzauka monga m'phiri la Perazimu, nadzakwiya monga m'cigwa ca Gibeoni; kuti agwire nchito yace, nchito yace yacilendo, ndi kuti acite cocita cace, cocita cace cacilendo.
22 Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za cionongeko cotsimikizidwa pa dziko lonse lapansi.
23 Cherani inu makutu, imvani mau anga; mverani, imvani kulankhula kwanga.
24 Kodi mlimi amalimabe kuti abzale? kodi amacocolabe, ndi kuswa zibuma za nthaka?
25 Atakonza tyatyatya pamwamba pace, kodi safesa ponse mawere, ndi kumwazamwaza citowe, nafesa tirigu m'mizere ndi barele m'malo ace osankhika, ndi mcewere m'maliremo?
26 Pakuti Mulungu wace amlangiza bwino namphunzitsa.
27 Pakuti sapuntha mawere ndi copunthira cakuthwa, ngakhale kuzunguniza njinga ya gareta pacitowe; koma amakulunga mawere ndi munsi, naomba citowe ndi cibonga.
28 Tirigu wa mkate aperedwa; pakuti samampuntha osaleka; ngakhale kuyendetsapo njinga ya gareta wace, ngakhale kumphwanya ndi ziboda za akavalo ace sapera.
29 Icinso cifumira kwa Yehova wa makamu, uphungu wace uzizwitsa ndi nzeru yace impambana.