1 Yimba, iwe wouma, amene sunabala; yimba zolimba ndi kupfuula zolimba, iwe amene sunabala mwana; pakuti ana a mfedwa acuruka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.
2 Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsaru za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.
3 Pakuti iwe udzafalikira ponse pa dzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandira amitundu colowa cao, ndi kukhalitsa anthu m'mabwinja.
4 Usaope, pakuti sudzakhala ndi manyazi; usasokonezedwe, pakuti sudzacitidwa manyazi; pakuti udzaiwala manyazi a ubwana wako, ndi citonzo ca umasiye wako sudzacikumbukiranso.
5 Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lace; ndi Woyera wa Israyeli ndiye Mombolo wako; Iye adzachedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.
6 Pakuti Yehova wakuitana iwe monga mkazi wakusiyidwa ndi wosauka m'mzimu, ngakhale mkazi wa ubwana wocotsedwa, ati Mulungu wako.
7 Kamphindi kakang'ono ndakusiya iwe, koma ndi cifundo cambiri ndidzakusonkhanitsa.
8 M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa cikhalire ndidzakucitira cifundo, ati Yehova Mombolo wako.
9 Pakuti kumeneku kuli kwa Ine monga madzi a Nowa; pakuti monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso pa dziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula.
10 Pakuti mapiri adzacoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakucokera iwe, kapena kusunthika cipangano canga ca mtendere, ati Yehova amene wakucitira iwe cifundo.
11 Iwe wosautsidwa, wobelukabeluka ndi namondwe, wosatonthola mtima, taona, ndidzakhazika miyala yako m'maanga-maanga abwino, ndi kukhazika maziko ako ndi masafiro.
12 Ndipo ndidzamanga mazenera ako ndi miyala yofiira, ndi zipata zako ndi bareketi, ndi malire ako onse ndi miyala yokondweretsa.
13 Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.
14 M'cilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutari ndi cipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutari ndi mantha, pakuti sadzafika cifupi ndi iwe.
15 Taona, iwo angasonkhanitse pamodzi, koma si ndi Ine; amene ali yense adzasonkhana pamodzi akangane ndi iwe adzagwa cifukwa ca iwe.
16 Taona, ndalenga wacipala amene abvukuta moto wamakala, ndi kuturutsamo cida ca nchito yace; ndipo ndalenga woononga kuti apasule.
17 Palibe cida cosulidwira iwe cidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'ciweruzo udzalitsutsa. Ici ndi colowa ca atumiki a Yehova, ndi cilungamo cao cimene cifuma kwa Ine, ati Yehova.