Yesaya 60 BL92

Ulemerero wa Yerusalemu ubwezedwa

1 Nyamuka, wala, pakuti kuunika kwake kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakuturukira.

2 Pakuti taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakuturukira, ndi ulemerero wace udzaoneka pa iwe.

3 Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kuturuka kwake,

4 Tukula maso ako uunguze-unguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako amuna adzacokera kutari, ndi ana ako akazi adzaleredwa pambali.

5 Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, cuma ca amitundu cidzafika kwa iwe.

6 Gulu la ngamila lidzakukuta, ngamila zazing'ono za Midyani ndi Efa; iwo onsewo adzacokera ku Seba adzabwera nazo golidi ndi zonunkhira; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.

7 Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebaioti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa pa guwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.

8 Ndani awa amene auluka ngati mtambo, ndi monga nkhunda ku mazenera ao?

9 Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisi kutenga ana ako amuna kutari, golidi wao ndi siliva wao pamodzi nao, cifukwa ca dzina la Yehova Mulungu wako, ndi cifukwa ca Woyera wa Israyeli, popeza Iye wakukometsa iwe.

10 Ndipo alendo adzamanga malinga ako, ndi mafumu ao adzakutumikira; pakuti m'kukwiya kwanga ndinakantha, koma mokomera mtima ndidakucitira iwe cifundo.

11 Zipata zako zidzakhalabe zotseguka, sizidzatsekedwa usana pena usiku, kuti abwere naco kwa iwe cuma ca amitundu, ndi mafumu ao otsogozedwa nao pamodzi.

12 Pakuti mtundu ndi ufumu umene udzakana kukutumikira udzaonongeka; inde mitundu imeneyo idzasakazidwa ndithu.

13 Ulemerero wa Lebano udzafika kwa iwe; mtengo wamlombwa, mtengo wamkuyu ndi mtengo wanaphini pamodzi, kukometsera malo a kacisi wanga; ndipo ndidzacititsa malo a mapazi anga ulemerero.

14 Ndipo ana amuna a iwo amene anabvuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakucepetsa iwe adzagwadira ku mapazi ako, nadzakucha iwe, Mudzi wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israyeli.

15 Ungakhale unasiyidwa ndi kudedwa, osapita munthu mwa iwe, Ine ndidzakusandutsa cangwiro cosatha, cokondweretsa ca mibadwo yambiri.

16 Iwe udzayamwanso mkaka wa amitundu, nudzayamwa bere la mafumu, nudzadziwa kuti Ine Yehova ndine mpulumutsi wako, ndi Mombolo wako, Wamphamvu wa Yakobo.

17 M'malo mwa mkuwa ndidzatenga golidi, ndi m'malo mwa citsulo ndidzatenga siliva, ndi m'malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m'malo mwa miyala ndidzatenga citsulo; ndidzakuikira akapitao a mtendere, ndi oyang'anira nchito a cilungamo.

18 Ciwawa sicidzamvekanso m'dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m'malire ako; koma udzacha malinga ako Cipulumutso, ndi zipata zako Matamando.

19 Dzuwa silidzakhalanso kuunika kwako usana, ngakhale mwezi sudzakuunikiranso kuti kuyere; koma Yehova adzakhala kwa iwe kuunika kosatha, ndi Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.

20 Dzuwa lako silidzalowanso, mwezi wako sudzanka kumidima; pakuti Yehova adzakhala kuunika kwako kosatha, ndi masiku a kulira maliro ako adzatha.

21 Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala colowa cao ku nthawi zonse, nthambi yooka Ine, nchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.

22 Wamng'ono adzasanduka cikwi, ndi wocepa adzasanduka mtundu wamphamvu; Ine Yehova ndidzafulumiza ici m'nthawi yace.