1 Tsoka kwa iwo amene atsikira kunka ku Aigupto kukathandizidwa, natama akavalo; nakhulupirira magareta, pakuti ali ambiri, ndi okwera pa akavalo, pakuti ali a mphamvu zambiri; koma sayang'ana Woyera wa Israyeli, ngakhale kumfuna Yehova!
2 Koma Iyenso ali wanzeru, nadzatengera coipa, ndipo sadzabwezanso mau ace, koma adzaukira banja la ocita zoipa, ndi amene athandiza iwo akugwira nchito yoipa.
3 Koma Aaigupto ndiwo anthu, si Mulungu; ndi akavalo ao ali nyama, si mzimu; ndipo pamene Yehova adzatambasula dzanja lace, wothandiza adzapunthwa, ndi wothandizidwa adzagwa, ndipo iwo onse awiri pamodzi adzalephera.
4 Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yace, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupitikitsa, ngakhale kudzicepetsa wokha, cifukwa ca phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo ku phiri la Ziyoni, ndi kucitunda kwace komwe.
5 Monga mbalame ziuluka, motero Yehova wamakamu adzacinjiriza Yerusalemu; Iye adzacinjirikiza ndi kuupulumutsa, adzapitirapo ndi kuusunga.
6 Bwerani kwa Iye amene mwampandukira kolimba, ana a Israyeli inu.
7 Pakuti tsiku limenelo iwo adzataya munthu yense mafano ace asiliva, ndi mafano ace agolidi amene manja anu anu anawapanga akucimwitseni inu.
8 Pamenepo Asuri adzagwa ndi lupanga losati la munthu; ndi lupanga losati la anthu lidzammariza iye; ndipo iye adzathawa lupanga, ndi anyamata ace adzalamba.
9 Ndipo mwala wace udzacoka, cifukwa ca mantha, ndi akalonga ace adzaopa mbendera, ati Yehova, amene moto wace uli m'Ziyoni, ndi ng'anjo yace m'Yerusalemu.