Yesaya 21 BL92

Aneneratu za kugwa kwa Babulo

1 Katundu wa cipululu ca kunyanja. Monga akabvumvulu a kumwela apitirira, kufumira kucipululu ku dziko loopsya.

2 Masomphenya obvuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Media iwe; kuusa moyo kwace konse ndakutonthoza.

3 Cifukwa cace m'cuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndicita mantha sindingathe kuona.

4 Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; cizitezite cimene ndinacikhumba candisandukira kunthunthumira.

5 Iwo akonza pa gome lodyera, aika alonda, adya, namwa; ukani, akalonga inu, dzozani mafuta cikopa.

6 Pakuti Ambuye atero kwa ine, Muka, ika mlonda anene cimene aciona;

7 ndipo pamene iye anaona khamu, amuna apakavalo awiri awiri, khamu la aburu, khamu la ngamila, iye adzamvetsera ndi khama mosamalitsa.

8 Ndipo iye anapfuulitsa ngati mkango, Ambuye inu, ine ndiimabe pamwamba pa nsanja nthawi ya usana, ndipo ndiikidwa mu ulonda wanga usiku wonse;

9 ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apaakavalo awiri awiri. Ndipo iye anayankha nati, Babulo wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yace asweka, nagwa pansi.

10 Kuomba kwanga nanga, ndi za pa dwale langa: cimene ine ndinacimva kwa Yehova wa makamu Mulungu wa Israyeli, ndanena kwa inu.

Aneneratu za kuonongeka kwa Duma

11 Katundu wa Duma.Wina aitana kwa ine kucokera ku Seiri, Mlonda, nthawi yanji ya usiku? Mlonda, nthawi yanji ya usiku?

12 Mlonda anati, Kuli kuca, koma kukali usiku; mukafuna kufunsa, funsani, bwerani, idzani.

Za kuonongeka kwa Arabiya

13 Katundu wa pa Arabiya.M'nkhalango ya m'Arabiya mudzagona, inu makamu oyendayenda a Dedani.

14 Mucingamire akumva ludzu ndi madzi; okhala m'dziko la Tema ananka kukomana ndi othawa ndi cakudya cao.

15 Pakuti iwo anathawa malupanga, malupanga osololedwa, ndi mauta-olifuka ndi nkhondo yobvuta.

16 Pakuti Ambuye ana tero kwa ine, Cisanapite caka malinga ndi zaka za wolembedwa nchito ulemerero wonse wa Kedara udzagoma;

17 ndi otsala amauta, ngwazi za ana a Kedara zidzacepa, pakuti Yehova Mulungu wa Israyeli wanena.