Yesaya 62 BL92

Cikhalidwe cokoma ca Yerusalemu

1 Cifukwa ca Ziyoni sindidzakhala cete, ndi cifukwa ca Yerusalemu sindidzapuma, kufikira cilungamo cace cidzaturuka monga kuyera, ndi cipulumutso cace monga nyali yoyaka.

2 Ndipo amitundu adzaona cilungamo cako, ndi mafumu onse ulemerero wako; ndipo udzachedwa dzina latsopano, limene m'kamwa mwa Yehova mudzachula.

3 Iwe udzakhalanso korona wokongola m'dzanja la Yehova, korona wacifumu m'dzanja la Mulungu wako.

4 Iwe sudzachedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzachedwanso Bwinja; koma iwe udzachedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa.

5 Pakuti monga mnyamata akwatira namwali, momwemo ana ako amuna adzakukwama iwe; ndi monga mkwati akondwera ndi mkwatibwi, momwemo Mulungu wako adzakondwera nawe.

6 Ndaika alonda pa malinga ako, Yerusalemu; iwo sadzakhala cete usana pena usiku; inu akukumbutsa Yehova musakhale cete,

7 ndipo musamlole akhale cete, kufikira Iye atakhazikitsa naika Yerusalemu akhale tamando m'dziko lapansi.

8 Yehova analumbira pa dzanja lace lamanja, ndi mkono wace wamphamvu, Zoonadi, sindidzaperekanso tirigu wako akhale cakudya ca adani ako, ndipo alendo sadzamwa vinyo wako amene iwe unagwirira nchito;

9 koma iwo amene adzakolola adzadya ndi kutamanda Yehova; ndi iwo amene adzamchera adzamumwa m'mabwalo a kacisi wanga.

10 Pitani, pitani pazipata; konzani njira ya anthu; undani, undani khwalala; cotsani miyala, kwezani mbendera ya anthu.

11 Taonani, Yehova walalikira kufikira malekezero a dziko lapansi. Nenani kwa mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona cipulumutso cako cifika; taona mphotho yace ali nayo, ndi nchito yace iri pamaso pace.

12 Ndipo iwo adzawacha Anthu opatulika, Oomboledwa a Yehova; ndipo iwe udzachedwa Wofunidwa, Mudzi wosasiyidwa.