Yesaya 27 BL92

Munda wamphesa wa Yehova

1 Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lace lolimba ndi lalikuru ndi lamphamvu adzalanga nangumi njoka yotamanga, ndi nangumi njoka yopindika-pindika; nadzapha cing'ona cimene ciri m'nyanja.

2 Tsiku limenelo: munda wa mphesa wavinyo, yimbani inu za uwo.

3 Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.

4 Ndiribe ukali; ndani adzalimbanitsa lunguzi ndi minga ndi Ine kunkhondo? ndiziponde ndizitenthe pamodzi.

5 Kapena mlekeni, agwire mphamvu zanga, nacite nane mtendere; inde, acite nane mtendere.

6 M'mibadwo ikudzayo Yakobo adzamera mizu; Israyeli adzaphuka ndi kucita mphundu; ndipo iwo adzadzaza ndi zipatso pa dziko lonse lapansi.

7 Kodi Mulungu wakantha Yakobo, monga umo anawakanthira akumkanthawo? kapena kodi iye waphedwa malinga ndi kuphedwa kwa iwo amene anaphedwa ndi iye?

8 Munalimbana naye pang'ono, pamene munamcotsa; wamcotsa iye kuomba kwace kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.

9 Cifukwa cace, mwa ici coipa ca Yakobo cidzafafanizidwa, ndipo ici ndi cipatso conse cakucotsa cimo lace; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.

10 Pakuti mudzi wocingidwa uli pa wokha, mokhalamo mwa bwinja, ndi mosiyidwa ngati cipululu; mwana wa ng'ombe adzadya kumeneko, nadzagonako pansi, nadzamariza nthambi zace.

11 Ponyala nthambi zace zidzatyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; cifukwa cace Iye amene anawalenga sadzawacitira cisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.

12 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Yehova adzaomba tirigu wace, kucokera madzi a nyanja, kufikira ku mtsinje wa Aigupto, ndipo mudzakunkhidwa mmodzi, inu ana a Israyeli.

13 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, lipenga lalikuru lidzaombedwa; ndipo adzafika omwe akadatayika m'dziko la Asuri, ndi opitikitsidwa a m'dziko la Aigupto; ndipo adzapembedza Yehova m'phiri lopatulika la pa Yerusalemu.