1 Wolungama atayika, ndipo palibe munthu wosamalirapo; ndipo anthu acifundo atengedwa, palibe wolingalira kuti wolungama acotsedwa pa coipa cirinkudza.
2 Iye alowa mumtendere, iwo apuma pa mphasa zao, yense woyenda moongoka.
3 Koma sendererani kuno cifupi, inu ana amuna a watsenga, mbeu yacigololo ndi yadama.
4 Ndiye yani mudzikondweretsa momseka? Ndani mulikumyasamira kukamwa, ndi kumturutsira lilime? Kodi inu simuli ana akulakwa, mbeu yonama?
5 Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?
6 Pakuti pa miyala yosalala ya m'cigwa pali gawo lako; iyo ndiyo gawo lako; ndiyo imene unaitsanulirira nsembe yothira, ndi kupereka nsembe yaufa. Kodi ndidzapembedzedwa pa zinthu zimenezi?
7 Pamwamba pa phiri lalitaritari unayala mphasa yako; kumenekonso wakwera kukapereka nsembe.
8 Ndi kumbuyo kwa zitseko ndi mphuthu waimiritsa cikumbutso cako, pakuti wadzionetsa wekha kwa wina, wosati kwa Ine; ndipo wakwerako, wakuza mphasa yako, ndi kupangana nao pangano; unakonda mphasa yao kumene unaiona.
9 Ndipo unanka kwa mfumu, utadzola mafuta ndi kucurukitsa zonunkhira zako; ndipo unatumiza atumwi ako kutari; ndipo wadzicepetsa wekha kufikira kunsi ku manda.
10 Unatopa ndi njira yako yaitari; koma sunanene, Palibe ciyembekezo; iwe wapeza moyo wa dzanja lako; cifukwa cace sunalefuka.
11 Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kucita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhala cete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiopa Ine konse?
12 Ndidzaonetsa cilungamo cako ndi nchito zako sudzapindula nazo.
13 Pamene pakupfuula iwe akupulumutse amene unawasonkhanitsa; koma mphepo idzawatenga, mpweya udzacotsa onse; koma iye amene andikhulupirira Ine adzakhala ndi dziko, nadzakhala naco colowa m'phiri langa lopatulika.
14 Ndipo adzanena, Undani, undani, konzani njira, cotsani cokhumudwitsa m'njira mwa anthu anga.
15 Pakuti atero Iye amene ali wamtari wotukulidwa, amene akhala mwacikhalire, amene dzina lace ndiye Woyera, Ndikhala m'malo atari ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzicepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzicepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
16 Pakuti sindidzatsutsana ku nthawi zonse, sindidzakwiya masiku onse; pakuti mzimu udzalefuka pamaso pa Ine, ndi miyoyo imene ndinailenga.
17 Cifukwa ca kuipa kwa kusirira kwace ndinakwiya ndi kummenya iye; ndinabisa nkhope yanga, ndipo ndinakwiya; ndipo iye anankabe mokhota m'njira ya mtima wace.
18 Ndaona njira zace, ndipo ndidzamciritsa; ndidzamtsogoleranso, ndi kumbwezera iye ndi olira maliro ace zotonthoza mtima.
19 Ndilenga cipatso ca milomo, Mtendere, mtendere kwa iye amene ali kutari, ndi kwa iye amene ali cifupi, ati Yehova; ndipo ndidzamciritsa iye.
20 Koma oipa ali ofanana ndi nyanja yowinduka; pakuti siingapume, ndi madzi ace autsa matope ndi ubve.
21 Palibe mtendere, ati Mulungu wanga, kwa oipa.