Yesaya 50 BL92

Mtumiki wa Yehova anyozedwa koma athandizidwa

1 Atero Yehova, Kalata wa cilekaniro ca amako ali kuti amene ndinamsudzula naye? pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona cifukwa ca zoipa zanu munagulitsidwa, ndi cifukwa ca kulakwa kwanu amanu anacotsedwa.

2 Cifukwa canji ndinafika osapeza munthu? ndi kuitana koma panalibe wina woyankha? Kodi dzanja langa lafupika konse, kuti silingathe kuombola? pena Ine kodi ndilibe mphamvu zakupulumutsa? Taona pa kudzudzula kwanga ndiumitsa nyanja yaikuru, ndi kusandutsa mitsinje cipululu; nsomba zace zinunkha cifukwa mulibe madzi, nizifa ndi ludzu.

3 Ndibveka thambo ndi kuda, ndi kuyesa ciguduli copfunda cace.

4 Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akucirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi im'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.

5 Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhala wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo.

6 Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisira nkhope yanga manyazi ndi kulabvulidwa.

7 Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata Ine; cifukwa cace sindinasokonezedwa; cifukwa cace ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi.

8 Iye ali pafupi amene alungamitsa Ine; ndani adzakangana ndi Ine? tiyeni tiimirire tonse pamodzi; mdani wanga ndani? andiyandikire.

9 Taonani, Ambuye Yehova adzathandiza Ine; ndani amene adzanditsutsa? taonani, iwo onse adzatha ngati cobvala, njenjete zidzawadya.

10 Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wace? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wace.

11 Taonani, inu nonse amene muyatsa moto, amene mudzimangira m'cuuno ndi nsakali, yendani inu m'cirangati ca moto wanu, ndi pakati pa nsakali zimene mwaziyatsa. Ici mudzakhala naco ca pa dzanja langa; mudzagona pansi ndi cisoni.