Yesaya 46 BL92

Aneneratu za kupasuka kwa mafano a ku Babulo

1 Beli agwada pansi, Nebo awerama; mafano ao ali pa zoweta, ndi pa ng'ombe; zinthu zimene inu munanyamula ponseponse ziyesedwa mtolo, katundu wakulemetsa nyama.

2 Milunguyo iwerama, igwada pansi pamodzi; singapulumutse katundu, koma iyo yeni yalowa m'ndende.

3 Mverani Ine, banja la Yakobo, ndi otsala onse a banja la Israyeli, amene ndakunyamulani kuyambira m'mimba, ndi kukusenzani cibadwire;

4 ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.

5 Kodi mudzandifanizira ndi yani, ndi kundilinganiza ndi kundiyerekeza, kuti ife tifanane?

6 Amene ataya golidi, namturutsa m'thumba, ndi kuyesa siliva ndi muyeso, iwo alemba wosula golidi; iye napanga nazo mlungu; iwo agwada pansi, inde alambira.

7 Iwo amanyamula mlunguwu paphewa, nausenza, naukhazika m'malo mwace, nukhala ciriri; pamalo pacepo sudzasunthika; inde, wina adzaupfuulira, koma sungathe kuyankha, kapena kumpulumutsa m'zobvuta zace.

8 Kumbukirani ici, nimucirimike, mudzikumbutsenso, olakwa inu.

9 Kumbukirani zinthu zoyamba zakale, kuti Ine ndine Mulungu, ndipo palibenso wina; Ine ndine Yehova, ndipo palibenso wina wofana ndi Ine;

10 ndilalikira za cimariziro kuyambira paciyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanacitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzacita zofuna zanga zonse;

11 ndiitana mbalame yolusa kucokera kum'mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kucokera ku dziko lakutari; inde, ndanena, ndidzacionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzacicitanso.

12 Mverani Ine, inu olimba mtima, amene muli kutari ndi cilungamo;

13 ndiyandikizitsa cifupi cilungamo canga sicidzakhala patari, ndipo cipulumutso canga sicidzacedwa; ndipo ndidzaika cipulumutso m'Ziyoni, ca kwa Israyeli ulemerero wanga.