Yesaya 38 BL92

Kudwala kwa Hezekiya ndi kuciritsidwa kwace

1 Masiku amenewo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Ndipo Yesaya mneneri, mwana wa Amozi, anadza kwa iye, nati kwa iye, Atero Yehova, Konza nyumba yako, pakuti iwe udzafa, sudzakhala ndi moyo.

2 Ndipo Hezekiya analoza nkhope yace kukhoma, napemphera kwa Yehova, nati,

3 Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndacita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.

4 Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yesaya, ndi kuti,

5 Ukanene kwa Hezekiya, Atero Yehova, Mulungu wa Davide, kholo lako, Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzaonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu.

6 Ndipo ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'manja mwa mfumu ya Asuri, ndipo ndidzacinjiriza mudzi uno.

7 Ndipo ici cidzakhala cizindikilo kwa iwe cocokera kwa Yehova, kuti Yehova adzacita ici wanenaci;

8 taona, ndidzabweza mthunzi wa pamakwerero, umene watsika pa makwerero a Ahazi ndi dzuwa, ubwerere makwerero khumi. Ndipo dzuwa linabwerera makwerero khumi pamakwerero, pamene udatsika mthunziwo.

9 Malemba a Hezekiya mfumu ya Ayuda muja anadwala, atacira nthenda yace.

10 Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m'zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.

11 Ndinati, Sindidzaona Yehova m'dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno;

12 Pokhala panga pacotsedwa, pandisunthikira monga hema wambusa;Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba;Iye adzandidula ine poomberapo;Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.

13 Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anatyolatyola mafupa anga onse;Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.

14 Ndinalankhula-lankhula ngati namzeze, pena cumba;Ndinalira maliro ngati nkhunda;Maso anga analephera pogadamira kumwamba.Yehova ndasautsidwa, mundiperekere cikoli.

15 Kodi ndidzanena ciani?Iye wanena kwa ine, ndiponso Iye mwini wacita ici;Ine ndidzayenda cete zaka zanga zonse,Cifukwa ca zowawa za moyo wanga.

16 Ambuye ndi zinthu izi anthu akhala ndi moyo.Ndipo m'menemo monse muli moyo wa mzimu wanga;Cifukwa cace mundiciritse ine,Ndi kundikhalitsa ndi moyo.

17 Taonani, ndinali ndi zowawa zazikuru,Cifukwa ca mtendere wanga;Koma Inu mokonda moyo wanga,Munaupulumutsa m'dzanja la cibvundi,Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu macimo anga onse.

18 Pakuti kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu;Imfa singakulemekezeni;Otsikira kudzenje sangaziyembekeze zoona zanu.

19 Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero;Atate adzadziwitsa ana ace zoona zanu.

20 Yehova ndiye wondipulumutsa ine;Cifukwa cace tidzayimba nyimbo zanga, ndi zoyimba zazingweMasiku onse a moyo wathu m'nyumba ya Yehova.

21 Ndipo Yesaya adati, Atenge mbulu wankhuyu, auike papfundo, Ndipo iye adzacira.

22 Hezekiya anatinso, Cizindikilo nciani, kuti ndidzakwera kunka ku nyumba ya Yehova?