Yesaya 25 BL92

Nvimbo yakulemekeza cifundo ca Mulungu

1 Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga, ndidzakukuzani Inu, ndidzatamanda dzina lanu, cifukwa mwacita zinthu zodabwitsa, ngakhale: zauphungu zakale, mokhulupirika ndi m'zoonadi.

2 Cifukwa Inu mwasandutsa mudzi muunda; mudzi walinga bwinja; nyumba ya alendo kuti isakhale mudzi; sudzamangidwa konse.

3 Cifukwa cace anthu amphamvu adzakulemekezani Inu, mudzi wa mitundu yakuopsya udzakuopani Inu.

4 Cifukwa Inu mwakhala linga la aumphawi, linga la osowa m'kubvutidwa kwace, pobisalira cimphepo, mthunzi wa pa dzuwa, pamene kuomba kwa akuopsya kufanana ndi cimphepo cakuomba chemba.

5 Monga kutentha m'malo ouma, Inu mudzaletsa phokoso la alendo; nyimbo ya akuopsya idzaletseka, monga mthunzi uletsa dzuwa.

6 Ndipo m'phiri limendi Yehova wa makamu adzakonzera anthu ace onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okha okha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.

7 Ndipo Iye adzaononga m'phiri limeneli cophimba nkhope cobvundikira mitundu yonse ya anthu, ndi nsaru yokuta amitundu onse.

8 Iye wameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo citonzo ca anthu ace adzacicotsa pa dziko lonse lapansi; cifukwa Yehova wanena.

9 Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; tamlindirira Iye, adzatipulumutsa; uyu ndiye Yehova, tamlindirira Iye, tidzakondwa ndikusekereram'cipulumutso cace.

10 Cifukwa m'phiri limeneli dzanja la Yehova lidzakhalamo, ndipo Moabu adzaponderezedwa pansi m'malo ace, monga maudzu aponderezedwa padzala.

11 Ndipo iye adzatambasula manja ace pakati pamenepo, monga wosambira atambasula manja ace posambira; koma Iye adzagwetsa pansi kunyada kwace, pamodzi ndi kunyenga kwa manja ace.

12 Ndipo linga la pamsanje la macemba ako Iye waligwetsa, naligonetsa pansi, nalifikitsa padothi, ngakhale papfumbi.