Yesaya 2 BL92

Ulemerero wa Israyeli m'tsogolomo, maweruzo a Mulungu pakatipo

1 Mau amene Yesaya mwana wa Amozi anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu.

2 Ndipo padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, ndipo lidzakwezedwa pamwamba pa zitunda; mitundu yonse idzasonkhana kumeneko.

3 Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zace, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ace; cifukwa m'Ziyoni mudzaturuka cilamulo, ndi mau a Yehova kucokera m'Yerusalemu.

4 Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.

5 Inu a nyumba ya Yakobo, tiyeni, tiyende m'kuwala kwa Yehova.

6 Cifukwa inu mwasiya anthu anu a nyumba ya Yakobo, cifukwa kuti iwo adzazidwa ndi miyambo ya kum'mawa, ndipo ali olaula ngati Afilisti, naomba m'manja ndi ana a acilendo.

7 Dziko lao ladzala siliva ndi golidi, ngakhale cuma cao ncosawerengeka; dziko lao lidzalanso akavalo, ngakhale magareta ao ngosawerengeka.

8 Dziko lao ladzalanso mafano; iwo apembedza nchito ya manja ao ao, imene zala zao zao zinaipanga.

9 Munthu wacabe agwada pansi, ndi munthu wamkuru adzicepetsa, koma musawakhululukire.

10 Lowa m'phanga, bisala m'pfumbi, kucokera pa kuopsya kwa Yehova, ndi pa ulemerero wacifumu wace.

11 Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.

12 Cifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa;

13 ndi pa mitengo yonse yamkungudza ya Lebano, yaitari ndi yotukulidwa, ndi pa mitengo yonse yathundu ya Basana;

14 ndi pa mapiri onse atari, ndi pa zitunda zonse zotukulidwa;

15 ndi pa nsanja zazitari zonse, ndi pa macemba onse;

16 ndi pa ngalawa zonse za Tarisi, ndi pa zithunzithunzi zonse zokondweretsa.

17 Ndipo kudzikweza kwa munthu kudzaweramitsidwa pansi, kudzikuza kwa munthu kudzatsitsidwa; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.

18 Ndimo mafano adzapita psiti.

19 Anthu adzalowa m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'maenje apansi, kuthawa kuopsya kwa Yehova, ndi ulemerero wacifumu wace, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu.

20 Tsiku limenelo munthu adzataya ku mfuko ndi ku mileme mafano ace asiliva ndi agolidi amene anthu anampangira iye awapembedze;

21 kuti akalowe m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'mindala a m'miyala, kuthawa kuopsya kwa Yehova, ndi ulemerero wacifumu wace, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu,

22 Siyani munthu, amene mpweya wace uli m'mphuno mwace; cifukwa m'mene awerengedwamo ndi muti?