Yesaya 29 BL92

Aneneratu za kulangidwa kwa Yuda wosakhulupirika, komanso za cipulumutso cace

1 Eya Arieli, Arieli, mudzi umene Davide anamangapo zithando! oniezerani caka ndi caka; maphwando afikenso;

2 pamenepo ndidzasautsa Arieli, ndipo padzakhala maliro ndi kulira; koma iye adzakhala kwa Ine monga Arieli.

3 Ndipo ndidzamanga zithando kuzungulira iwe ponse, ndipo ndidzamanga linga ndi kuunjika miulu yakumenyanirana ndi iwe.

4 Ndipo iwe udzagwetsedwa pansi, nudzanena uli pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala pansi koturuka m'pfumbi; ndi mau ako adzakhala ngati a wina amene ali ndi mzimu wobwebweta, kucokera pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala konong'ona kocokera m'pfumbi,

5 Koma khamu la acilendo ako lidzafanana ndi pfumbi losalala, ndi khamu la oopsya lidzakhala monga mungu wocokacoka; inde kudzaoneka modzidzimuka dzidzidzi.

6 Ndipo Yehova wa makamu adzamzonda ndi bingu, ndi cibvomezi, ndi mkokomo waukuru, kabvumvulu, ndi mkuntho, ndi lawi la moto wonyambita.

7 Ndipo khamu la mitundu yonse yomenyana ndi Arieli, ngakhale yonse yomenyana naye ndi linga lace, ndi kumsautsa idzafanana ndi loto, masomphenya a usiku.

8 Ndipo kudzafanana ndi munthu wanjala, pamene alota, ndipo, taonani, akudya; koma auka, ndipo m'kati mwace muli zi; kapena monga munthu waludzu pamene alota, ndipo, taonani, akumwa; koma auka ndipo taonani walefuka, ndipo m'kati mwace muli gwa; momwemo lidzakhala khamu la mitundu yonse yomenyana ndi phiri la Ziyoni.

9 Khalani ndi kudabwa; sangalalani ndi kukhala akhungu; iwo aledzera, koma si ndi vinyo, ali dzandi dzandi; koma si ndi cakumwa caukali.

10 Pakuti Yehova watsanulira pa inu mzimu wa tulo togonetsa, natseka maso anu, ndiwo aneneri; naphimba mitu yanu, ndiwo alauli.

11 Ndipo masomphenya onse akusandukirani mau a m'buku limatidwa ndi phula, limene anthu amapereka kwa wina wodziwa kuwerenga, nati, Werengani umu; koma ati, Sindingathe, cifukwa lamatidwa ndi phula;

12 ndipo buku laperekedwa kwa wosadziwa kuwerenga, ndi kuti, Werengani umu; koma ati, Ine sindinaphunzira.

13 Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutari ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;

14 cifukwa cace, taonani, ndidzacitanso mwa anthu awa nchito yodabwitsa, ngakhale nchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu ao anzeru idzatha, ndi luntha la anthu ao ozindikira lidzabisika.

15 Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi nchito zao ziri mumdima, ndipo amati Ndani ationa ife? ndani atidziwa ife?

16 Ozolitsa inu! Kodi woumba adzayesedwa ngati dothi; kodi cinthu copangidwa cinganene za iye amene anacipanga, Iye sanandipanga ine konse; kapena kodi cinthu coumbidwa cinganene za iye amene anaciumba, Iye alibe nzeru?

17 Kodi sikatsala kamphindi kakang'ono, ndipo Lebano adzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango?

18 Ndipo tsiku limenelo gonthi adzam va mau a m'buku, ndi maso akhungu adzaona poturuka m'zoziya ndi mumdima.

19 Ofatsanso kukondwa kwao kudzacuruka mwa Yehova, ndi aumphawi a mwa anthu adzakondwerera mwa Woyera wa Israyeli.

20 Pakuti woopsya wagoma, ndi wonyoza watha, ndi onse odikira zolakwa alikhidwa;

21 amene apalamulitsa munthu mlandu, namchera msampha iye amene adzudzula pacipata, nambweza wolungama ndi cinthu cacabe.

22 Cifukwa cace Yehova amene anaombola Abrahamu, atero za banja la Yakobo: Yakobo sadzakhala ndi manyazi tsopano, ngakhale nkhope yace tsopano sidzagwa.

23 Koma pamene iye aona ana ace, nchito ya manja anga, pakati pa iye, iwo adzayeretsa dzina langa; inde, iwo adzayeretsa Woyera wa Yakobo, nadzaopa Mulungu wa Israyeli.

24 Iwonso osocera mumzimu adzadziwa luntha, ndi iwo amene ang'ung'udza adzaphunzitsidwa.