Yesaya 58 BL92

Kusala kosayenera, ndi kusala koyenera

1 Pfuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga colakwa cao, ndi banja la Yakobo macimo ao.

2 Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ocita cilungamo, osasiya cilangizo ca Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu.

3 Amati, Bwanji ife tasala kudya, ndipo Inu simuona? ndi bwanji ife tabvutitsa moyo wathu, ndipo Inu simusamalira? Taonani, tsiku la kusala kudya kwanu inu mupeza kukondwerera kwanu, ndi kutsendereza anchito anu onse.

4 Taonani, inu musala kudya kuti mukangane ndi kutsutsana ndi kukantha ndi nkhonya yoipa; inu simusala kudya tsiku lalero kuti mumveketse mau anu kumwamba.

5 Kodi kusala kudya koteroko ndiko ndinakusankha? tsiku lakubvutitsa munthu moyo wace? Kodi ndiko kuweramitsa mutu wace monga bango, ndi kuyala ciguduli ndi phulusa pansi pace? Kodi uyesa kumeneko kusala kudya, ndi tsiku lobvomerezeka kwa Yehova?

6 Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga gori, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti mutyole magori onse?

7 Kodi si ndiko kupatsa cakudya cako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? pakuona wamalisece kuti umbveke, ndi kuti usadzibisire wekha a cibale cako?

8 Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kucira kwako kudzaonekera msanga msanga; ndipo cilungamo cako cidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wocinjiriza pambuyo pako.

9 Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzapfuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati ucotsa pakati pa iwe gori, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa,

10 ndipo ngati upereka kwa wanjala cimene moyo Iwako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wobvutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;

11 ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'cirala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ace saphwa konse.

12 Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a mibadwo yambiri; udzachedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira zakukhalamo.

13 Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kucita kukondwerera kwako tsiku: langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osacita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha;

14 pomwepo udzakondwa mwa Yehova; ndipo Ine ndidzakuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi; ndipo ndidzakudyetsa colowa ca kholo lako Yakobo; pakuti pakamwa pa Yehova pananenapo.