Yesaya 23 BL92

Kupasuka ndi kumangidwanso kwa Turo

1 Katundu wa Turo.Kuwani, inu ngalawa za Tarisi; cifukwa wapasudwa, kulibenso nyumba, kulibe polowera; kucokera ku dziko la Kitimo kwabvumbulutsidwa kwa iwo.

2 Khalani cete, inu okhala m'cisumbu; iwe amene anakudzazanso amalonda a ku Zidoni, opita m'nyanja.

3 Ndi pa nyanja zazikuru anapindula ndi mbeu za ku Sihori ndizo dzinthu za ku Nile; ndi kumeneko kunali msika wa amitundu.

4 Khala ndi manyazi, iwe Zidoni; cifukwa nyanja yanena, linga la kunyanja, ndi kuti, Ine sindinamve zowawa, kapena kubala, kapena kulera anyamata, kapena kulera anamwali.

5 Pofika mbiriyo ku Aigupto, iwo adzamva kuwawa kwambiri pa mbiri ya Turo.

6 Olokani inu, kunka ku Tarisi, kuwani, inu okhala m'cisumbu.

7 Kodi umene ndi mudzi wanu wokondwa, wacikhalire kale lomwe, umene mapazi ace anaunyamula kunka nao kutari kukhalako?

8 Ndani wapanga uphungu uno pa Turo, mudzi umene upereka akorona, amalonda ace ali akalonga, ogulitsa ace ali olemekezeka pa dziko lapansi?

9 Yehova wa makamu wapanga uphungu uwu, kuipitsa kunyada kwa ulemerero wonse, kupepula onse olemekezeka a m'dziko lapansi.

10 Pita pakati pa dziko lako monga Nile, iwe mwana wamkazi wa Tarisi; palibenso lamba.

11 Iye watambasula dzanja lace panyanja, wagwedeza maufumu; Yehova walamulira za amalonda, kupasula malinga ace.

12 Ndipo Iye anati, Iwe sudzakondwanso konse, iwe namwali wobvutidwa, mwanawamkazi wa Zidoni; uka, oloka kunka ku Kitimu; ngakhale kumeneko iwe sudzapumai.

13 Taonani, dziko la Akasidi; anthu awa sakhalanso; Asuri analiika ilo likhale la iwo okhala m'cipululu; iwo amanga nsanja zao, nagumula nyumba za mafumu ace; nalipasula.

14 Kuwani, inu ngalawa za Tarisi; pakuti linga lanu lapasulidwa.

15 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti Turo adzaiwalika zaka makumi asanu ndi awiri, malinga ndi masiku a mfumu imodzi; zitapita zaka makumi asanu ndi ziwirizo, cidzakhala kwa Turo monga m'nyimbo ya mkazi wadama.

16 Tenga mngoli, yendayenda m'mudzi, iwe mkazi wadama, amene unaiwalika; yimba zokoma, curukitsa nyimbo, kuti ukumbukiridwe.

17 Ndipo padzali, zitapita zaka makumi asanu ndi awirizo, kuti Yehova adzazonda Turo, ndipo iye adzabwerera ku mphotho yace, nadzacita dama ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala kunja kuno.

18 Malonda ace ndi mphotho yace zidzakhala zopatulikira Yehova; sizidzasungidwa kapena kuikidwa; cifukwa malonda ace adzakhala kwa iwo, amene akhala pamaso pa Yehova, kuti adye mokwana, nabvale caulemu.