Yesaya 53 BL92

Masomphenya a cisauko ndi ulemerero wa Mtumiki wa Yehova

1 Ndani wamvera uthenga wathu? Ndi mkono wa Yehova wabvumbulukira yani?

2 Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pace ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m'nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe.

3 Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeza.

4 Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuvesa wokhomedwa wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wobvutidwa.

5 Koma Iye analasidwa cifukwa ca zolakwa zathu, natundudzidwa cifukwa ca mphulupulu zathu; cilango cotitengera ife mtendere cinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yace ife taciritsidwa.

6 Tonse tasocera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.

7 Iye anatsenderezedwa koma anadzicepetsa yekha osatsegula pakamwa pace; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwana wa nkhosa amene ali du pamaso pa omsenga, motero sanatsegula pakamwa pace.

8 Anacotsedwa ku cipsinjo ndi ciweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wace? pakuti walikhidwa kunja kuno; cifukwa ca kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa.

9 Ndipo anaika manda ace pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yace, ngakhale Iye sanacita ciwawa, ndipo m'kamwa mwace munalibe cinyengo.

10 Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wace ukapereka nsembe yoparamula, Iye adzaona mbeu yace, adzatanimphitsa masiku ace; ndipo comkondweretsa Yehova cidzakula m'manja mwace.

11 Iye adzaona zotsatira mabvuto a moyo wace, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zace mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.

12 Cifukwa cace ndidzamgawira gawo ndi akuru; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wace kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula macimo a ambiri, napembedzera olakwa.