1 Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wacifumu, ndi dziko lapansi ndi coikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?
2 Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.
3 Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwana wa nkhosa alingana ndi wotyola khosi la garu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza conunkhira akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zao zao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;
4 Inenso ndidzasankha zodzinyenga nazo, ndipo ndidzatengera mantha ao pa iwo; pakuti pamene ndinaitana, panalibe woyankha; pamene ndinalankhula, iwo sanamva konse; koma anacita coipa m'maso mwanga, ndi kusankha cimene ndisanakondwere naco.
5 Imvani mau a Yehova, inu amene munthunthumira ndi mau ace; abale anu amene akudani inu, amene anaponya inu kunja cifukwa ca dzina langa, iwo anati, Yehova alemekezedwe, kuti ife tione kusangalala kwanu; koma iwo adzakhala ndi manyazi.
6 Mau a phokoso acokera m'mudzi, mau ocokera m'Kacisi, mau a Yehova amene abwezera adani ace cilango.
7 Mkazi asanamve zowawa, anabala mwana; kupweteka kwace kusanadze, anabala mwana wamwamuna.
8 Ndani anamva kanthu kotereko? ndani anaona zinthu zoterezo? Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa? pakuti pamene Ziyoni anamva zowawa, pomwepo anabala ana ace.
9 Kodi Ine ndidzafikitsira mkazi nthawi yakutula osamtulitsa? ati Yehova; kodi Ine amene ndibalitsa ndidzatseka mimba? ati Mulungu wako.
10 Sangalalani inu pamodzi ndi Yerusalemu, ndipo kondwani cifukwa ca iye, inu nonse amene mumkonda; sangalalani kokondwa pamodzi ndi iye, inu nonse akumlira maliro;
11 kuti mukayamwe ndi kukhuta ndi mabere a zitonthozo zace; kuti mukafinye mkaka ndi kukondwerera ndi unyinji wa ulemerero wace.
12 Pakuti atero Yehova, Taonani ndidzamfikitsira mtendere ngati mtsinje, ndi ulemerero wa amitundu ngati mtsinje wosefukira. Inu mudzayamwa, ndi kunyamulidwa pambali, ndi kululuzidwa pa maondo,
13 Monga munthu amene amace amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima m'Yerusalemu.
14 Ndipo mudzaciona, ndipo mtima wanu udzasangalala, ndipo mafupa anu adzakula ngati msipu; ndipo dzanja la Yehova lidzadziwika ndi atumiki ace, ndipo adzakwiyira adani ace.
15 Pakuti taonani, Yehova adzafika m'moto, ndi magareta ace adzafanana ndi kabvumvulu; kubwezera mkwiyo wace ndi ukali, ndi kudzudzula ndi malawi amoto,
16 Pakuti Yehova adzatsutsana ndi moto, ndi lupanga lace, ndi anthu onse; ndi ophedwa a Yehova adzakhala ambiri.
17 Iwo amene adzipatulitsa nadziyeretsa, kuti amuke kuminda tsatane tsatane, ndi kudya nyama ya nkhumba, ndi conyansa, ndi mbewa, adzathedwa pamodzi, ati Yehova.
18 Pakuti Ine ndidziwa nchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga.
19 Ndipo ndidzaika cizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisi, kwa Puli ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubali ndi Yavana, ku zisumbu zakutari, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.
20 Ndipo iwo adzatenga abale anu onse mwa amitundu onse akhale nsembe ya kwa Yehova; adzabwera nao pa akavalo, ndi m'magareta, ndi m'macila, ndi pa nyuru, ndi pa ngamila, kudza ku phiri langa lopatulika ku Yerusalemu, ati Yehova, monga ana a Israyeli abwera nazo nsembe zao m'cotengera cokonzeka ku nyumba ya Yehova.
21 Ndipo ena a iwo ndidzawatenga akhale ansembe ndi Alevi, ati Yehova.
22 Pakuti monga m'mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano limene ndidzalenga, lidzakhalabe pamaso pa Ine, ati Yehova, momwemo adzakhalabe ana anu ndi dzina lanu.
23 Ndipo kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira ku unzace, ndi kuyambira pa Sabata lina kufikira ku linzace, anthu onse adzafika kudzapembedzera pamaso pa Ine, ati Yehova.
24 Ndipo iwo adzaturuka ndi kuyang'ana mitembo ya anthu amene andilakwira Ine, pakuti mbozi yao sidzafa, pena moto wao sudzazimidwa; ndipo iwo adzanyansa anthu onse.