Yeremiya 1 BL92

Kuitanidwa kwa Yeremiya akhale mneneri

1 MAU a Yeremiya mwana wa Hilikiya, wa ansembe amene anali ku Anatoti m'dziko la Benjamini;

2 amene anamdzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wace wa Amoni, mfumu ya Ayuda caka cakhumi ndi citatu ca ufumu wace.

3 Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wace wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi cimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wacisanu.

4 Ndipo anadza kwa ine mau a Yehova, kuti,

5 Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.

6 Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! taonani, sindithai kunena pakuti ndiri mwana.

7 Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena conse cimene ndidzakuuza.

8 Usaope nkhope zao; cifukwa Ine ndiri ndi iwe kuti ndikulanditse iwe, ati Yehova.

9 Ndipo Yehova anaturutsa dzanja lace, na'khudza pakamwa panga; nati Yehova kwa ine, Taona ndaika mau anga m'kamwa mwako;

10 penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse; umange, ubzyale.

Masomphenya oyamba a Yeremiya

11 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Yeremiya, uona ciani? Ndipo ndinati, Ine ndiona ntyole ya katungurume.

12 Ndipo Yehova anati kwa ine, Waona bwino pakuti Ine ndidzadikira mau anga kuwacita.

13 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yaciwiri, kuti, ona ciani? Ndipo ndinati, Ine ndiona mphika wogaduka; ndi pakamwa pace unafulatira kumpoto.

14 Ndipo Yehova anati kwa ine, Kucokera kumpoto coipa cidzaturukira onse okhala m'dziko.

15 Pakuti, taona, ndidzaitana mabanja onse a maufumu a kumpoto, ati Yehova; ndipo adzafika nadzaika yense mpando wacifumu wace pa zipata za Yerusalemu, ndi pa malinga onse ozinga pamenepo, ndi pa midzi yonse ya Yuda.

16 Ndipo ndidzanena nao za maweruzo anga akuweruzira zoipa zao zonse; popeza anandisiya Ine, nafukizira milungu yina, nagwadira nchito za manja ao.

17 Koma iwe ukwinde m'cuuno mwako, nuuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usaope nkhope zao ndingakuopetse iwe pamaso pao.

18 Cifukwa, taona, ndakuyesa iwe lero mudzi walinga, mzati wacitsulo, makoma amkuwa, pa dziko lonse, ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akuru ace, ndi pa ansembe ace, ndi pa anthu a m'dziko.

19 Ndipo adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; cifukwa Ine ndiri ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.