1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,
2 Ima m'cipata ca nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.
3 Yehova wa makamu atero, Mulungu wa Israyeli, Konzani njira zanu ndi macitidwe anu, ndipo ndidzakukhalitsani inu m'malo ano.
4 Musakhulupirire mau onama, kuti, Kacisi wa Yehova, kacisi wa Yehova, kacisi wa Yehova ndi awa.
5 Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi macitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wace;
6 ndi kuleka kutsendereza mlendo, ndi wamasiye, ndi mkazi wamasiye, osakhetsa mwazi wosacimwa m'malo muno, osatsata milungu yina ndi kudziipitsa nayo;
7 ndipo ndidzakukhazikani inu m'malo muno, m'dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuyambira kale lomwe kufikira muyaya,
8 Taonani, mukhulupirira mau onama, osapindulitsa.
9 Kodi mudzapha, ndi kuba, ndi kucita cigololo, ndi kulumbira zonama, ndi kupereka nsembe kwa Baala, ndi kutsata milungu yina imene simunaidziwa,
10 ndi kudza ndi kuima pamaso panga m'nyumba yino, imene ichedwa dzina langa, ndi kuti, Talanditsidwa; kuti mucite zonyansa izi?
11 Kodi nyumba yino, imene ichedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu? Taona, Ine ndaciona, ati Yehova.
12 Koma pitani tsopano ku malo anga amene anali m'Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona cimene ndinacitira cifukwa ca zoipa za anthu anga Israyeli.
13 Ndipo tsopano, cifukwa munacita nchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamva; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankha;
14 cifukwa cace ndidzaicitira nyumba iyi, imene ichedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzacitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinacitira Silo.
15 Ndipo ndidzakucotsani inu pamaso panga, monga ndinacotsa abale anu onse, mbeu zonse za Efraimu.
16 Cifukwa cace iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mpfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe.
17 Kodi suona iwe cimene acicita m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu?
18 Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu yina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.
19 Kodi autsa mkwiyo wanga? ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao?
20 Cifukwa cace, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pa malo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.
21 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli; Ikani zopereka zopsereza zanu pa nsembe zophera zanu, nimudye nyama.
22 Pakuti sindinanena kwa makolo anu, tsiku lija ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, ngakhale kuwauza nsembe zopsereza kapena zophera;
23 koma cinthu ici ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti cikukomereni.
24 Koma sanamvera, sanachera khutu, koma anayenda m'upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera cambuyo osayenda m'tsogolo.
25 Ciyambire tsiku limene makolo anu anaturuka m'dziko la Aigupto kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo;
26 koma sanandimvera Ine, sanacherakhutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.
27 Ndipo uzinena kwa iwo mau awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe.
28 Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, coonadi catha, cadulidwa pakamwa pao.
29 Senga tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti se; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.
30 Pakuti ana a Yuda anacita coipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yochedwa dzina langa, kuti alipitse.
31 Namanga akacisi a ku Tofeti, kuli m'cigwa ca mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao amuna ndi akazi; cimene sindinauza iwo, sicinalowa m'mtima mwanga.
32 Cifukwa cace, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzachedwanso Tofeti, kapena Cigwa ca mwana wa Hinomu, koma Cigwa ca Kuphera; pakuti adzataya m'Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa.
33 Ndipo mitembo ya anthu awa idzakhala zakudya za mbalame za mlengalenga, ndi za zirombo za dziko lapansi; palibe amene adzaziopsa.
34 Ndipo ndidzaletsa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, mau akukondwa ndi mau akusekera, ndi mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi; pakuti dziko lidzasanduka bwinja.