Yeremiya 25 BL92

Atalangidwa Aisrayeli adzalangidwa amitundu ena omwe

1 Mau amene anadza kwa Yeremiya za anthu onse a Yuda caka cacinai ca Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda; ndico caka coyamba ca Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo;

2 amene Yeremiya ananena kwa anthu onse a Yuda, ndi onse okhala m'Yerusalemu, kuti:

3 Kuyambira caka cakhumi ndi citatu ca Yosiya mwana wace wa Amoni, mfumu ya Yuda, kufikira lero lomwe, zakazi makumi awiri ndi zitatu, mau a Yehova anafika kwa ine, ndipo ndanena kwa inu, pouka mamawa ndi kunona; koma simunamvera.

4 Ndipo Yehova watuma kwa inu atumiki ace onse ndiwo aneneri, pouka mamawa ndi kuwatuma; koma simunamvera, simunachera khutu lanu kuti mumve;

5 ndi kuti, Mubwerere tsopano nonsenu, yense kuleka njira yace yoipa, ndi zoipa za nchito zanu, ndi kukhala m'dziko limene Yehova anapatsa inu ndi makolo anu, kuyambira kale kufikira muyaya;

6 musatsate milungu yina kuitumikira, ndi kuigwadira, musautse mkwiyo wanga ndi nchito ya manja anu; ndingacitire inu coipa.

7 Koma simunandimvera Ine, ati Yehova; kuti muutse mkwiyo wanga ndi nchito ya manja anu ndi kuonapo coipa inu.

8 Cifukwa cace Yehova wa makamu atero: Popeza simunamvera mau anga,

9 taonani, Ine ndidzatuma ndi kutenga mabanja onse a kumpoto, ati Yehova, ndipo ndidzatuma kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga, ndipo ndidzatengera iwo pa dziko lino, ndi pa okhalamo ace onse, ndi pa mitundu iyi yozungulira, ndipo ndidzathetsa iwo ndithu, ndi kuwayesa iwo cizizwitso, ndi cotsonyetsa, ndi bwinja lamuyaya.

10 Ndiponso ndidzawacotsera mau akusekera ndi mau akukondwera, ndi mau a mkwati, ndi mau a mkwatibwi, mau a mphero, ndi kuwala kwa nyali.

11 Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja, ndi cizizwitso, ndipo mitundu iyi idzatumikira mfumu ya ku Babulo zaka makumi asanu ndi awiri.

12 Ndipo kudzakhala, zitapita zaka makumi asanu ndi awiri, ndzidzalanga mfumu ya ku Babulo, ndi mtundu uja womwe, ati Yehova, cifukwa ca mphulupulu zao, ndi dziko la Akasidi; ndipo ndidzaliyesa mabwinja amuyaya.

13 Ndipo ndidzatengera dzikolo mau anga onse amene ndinanenera ilo, mau onse olembedwa m'buku ili, amene Yeremiya wanenera mitundu yonse.

14 Pakuti mitundu yambiri ndi mafumu akuru adzayesa iwo atumiki ao; ndipo ndidzabwezera iwo monga mwa macitidwe ao, monga mwa nchito ya manja ao.

15 Pakuti Yehova, Mulungu wa Israyeli, atero kwa ine, Tenga cikho ca vinyo wa ukaliwu pa dzanja langa, ndi kumwetsa mitundu yonse, imene ndikutumizirako.

16 Ndipo adzamwa, nadzayenda dzandi dzandi, nadzacita misala, cifukwa ca lupanga limene Ine ndidzatumiza mwa iwo.

17 Ndipo ndinatenga cikho pa dzanja la Yehova, ndinamwetsa mitundu yonse, imene Yehova ananditumizirako;

18 Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, ndi mafumu ace omwe, ndi akuru ace, kuwayesa iwo bwinja, cizizwitso, cotsonyetsa, ndi citemberero; monga lero lino;

19 Farao mfumu ya ku Aigupto, ndi atumiki ace, ndi akuru ace, ndi anthu ace onse;

20 ndi anthu onse osanganizidwa, ndi mafumu onse a dziko la Uzi, ndi mafumu onse a dziko la Afilisti, ndi Asikeloni, ndi Gaza, ndi Ekroni, ndi otsala a Asdodi,

21 Edomu, ndi Moabu, ndi ana a Amoni,

22 ndi mafumu onse a Turo, ndi mafumu onse a Zidoni, ndi mafumu a cisumbu cimene ciri patsidya pa nyanja;

23 Dedani, ndi Tema, ndi Buzi, ndi onse amene ameta m'mbali mwa tsitsi;

24 ndi mafumu onse a Arabiya, ndi mafumu onse a anthu osanganizidwa okhala m'cipululu;

25 ndi mafumu onse a Zimiri, ndi mafumu onse a Elamu, ndi mafumu onse a Medi,

26 ndi mafumu onse a kumpoto, a kutari ndi a kufupi, wina ndi mnzace; ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala pansi pano; ndi mfumu ya Sesaki adzamwa pambuyo pao.

27 Ndipo uziti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Imwani inu, ndi kuledzera, ndi kusanza, ndi kugwa, osanyamukanso konse, cifukwa ca lupanga limene ndidzatumiza mwa inu.

28 Ndipo padzakhala, ngati akana kutenga cikho pa dzanja lako kuti amwe, uziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Kumwa muzimwa.

29 Pakuti, taonani, ndiyamba kucita coipa pa mudzi umene uchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m'dziko lapansi, ati Yehova wa makamu.

30 Cifukwa cace muwanenere iwo mau onse awa, ndi kuti kwa iwo, Yehova adzabangula kumwamba, nadzachula mau ace mokhalamo mwace moyera; adzabangulitsira khola lace; adzapfuula, monga iwo akuponda mphesa, adzapfuulira onse okhala m'dziko lapansi.

31 Phokoso lidzadza ku malekezero a dziko lapansi; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi mitundu ya anthu, adzatsutsana ndi anthu onse; koma oipa, adzawapereka kulupanga, ati Yehova.

32 Yehova wa makamu atero, Taonani, zoipa zidzaturuka ku mtundu kunka m'mitundu, ndipo namondwe adzauka kucokera ku malekezero a dziko lapansi.

33 Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kucokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dzikolapansi, sadzaliridwa maliro, sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka.

34 Kuwani, inu abusa, lirani, gubudukani, inu akuru a zoweta; pakuti masiku a kuphedwa kwanu akwanira ndithu, ndipo ndidzakuphwanyani inu, ndipo mudzagwa ngati cotengera cofunika.

35 Ndipo abusa adzasowa pothawira, mkuru wa zoweta adzasowa populumukira.

36 Mau akupfuula abusa, ndi kukuwa mkuru wa zoweta! pakuti Yehova asakaza busa lao.

37 Ndipo makola amtendere adzaonongeka cifukwa ca mkwiyo woopsa wa Yehova.

38 Wasiya ngaka yace, monga mkango; pakuti dziko lao lasanduka cizizwitso cifukwa ca ukali wa lupanga losautsa, ndi cifukwa ca mkwiyo wace waukali.