Yeremiya 49 BL92

Citsutso ca Aamoni

1 Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israyeli alibe ana amuna? alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi cifukwa canji, ndi anthu ace akhala m'midzi mwace?

2 Cifukwa cace, taonani, masiku afika, ati Yehova, Ine ndidzamveketsa mpfuu ya nkhondo yomenyana ndi Raba wa ana a Amoni; ndipo adzasanduka muunda wabwinja, ndipo ana ace akazi adzatenthedwa ndi moto; pamenepo Israyeli adzalanda iwo amene adamlanda, ati Yehova.

3 Kuwa, iwe Hesiboni, pakuti Ai wapasuka; lirani, inu ana akazi a Raba, mubvale ciguduli; citani maliro, thamangani kwina ndi kwina pamipanda; pakuti mfumu yao idzalowa m'ndende, ansembe ace ndi akuru ace pamodzi.

4 Cifukwa canji udzitamandira ndi zigwa, cigwa cako coyendamo madzi, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo, amene anakhulupirira cuma cace, nati, Adza kwa ine ndani?

5 Taona ndidzakutengera mantha, ati Ambuye, Yehova wa makamu, akucokera kwa onse amene akuzungulira iwe; ndipo mudzaingitsidwa yense kulozera maso ace, ndipo palibe amene adzasonkhanitsa osocera.

6 Koma pambuyo pace ndidzabwezanso undende wa ana a Amoni, ati Yehova.

Za kulangidwa kwa Aedomu

7 Za Edomu. Yehova wa makamu atero: Kodi m'Temani mulibenso nzeru? kodi uphungu wawathera akucenjera? kodi nzeru zao zatha psiti?

8 Thawani inu, bwerani, khalani mwakuya, inu okhala m'Dedani; pakuti ndidzatengera pa iye tsoka la Esau, nthawi yoti ndidzamlanga iye.

9 Akafika kwa inu akuchera mphesa, sadzasiya mphesa zokunkha? akafika usiku akuba, adzaononga mpaka kutha?

10 Pakuti ndambvula Esau, ndambvundukula, sadzatha kubisala; mbeu zace zaonongeka, ndi abale ace, ndi anansi ace, ndipo palibe iye.

11 Siya ana ako amasiye, Ine ndidzawasunga; akazi ako amasiye andikhulupirire Ine.

12 Pakuti Yehova atero: Taonani, iwo amene sanaweruzidwa kuti amwe cikho adzamwadi; kodi iwe ndiye amene adzakhala wosalangidwa konse? sudzakhala wosalangidwa, koma udzamwadi.

13 Pakuti ndalumbira, Pali Ine, ati Yehova, kuti Boma adzakhala cizizwitso, citonzo, copasuka, ndi citemberero; ndipo midzi yace yonse idzakhala yopasuka cipasukire.

14 Ndamva mthenga wa kwa Yehoya, ndipo mthenga watumidwa mwa amitundu, wakuti, Sonkhanani, mumdzere, nimuukire nkhondo.

15 Pakuti, caona, ndakuyesa iwe wamng'ono mwa amitundu, ndi wonyozedwa mwa anthu.

16 Koma za kuopsya kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa citunda, ngakhale usanja cisanja cako pamwamba penipeni ngati ciombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.

17 Ndipo Edomu adzakhala cizizwitso; ndipo yense wakupitapo adzazizwa, ndipo adzatsonyera zobvuta zace zonse.

18 Monga m'kupasuka kwa Sodomu ndi Gomora ndi midzi inzace, ati Yehova, munthu ali yense sadzakhala m'menemo, mwana wa munthu ali yense sadzagona m'menemo.

19 Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wocokera ku Yordano wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amcokere; ndipo ali yense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wace, pakuti wakunga Ine ndani? adzandiikira nthawi ndani? ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?

20 Cifukwa cace tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala m'Temani, ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.

21 Dziko lapansi linthunthumira ndi phokoso Ija kugwa kwao; pali mpfuu, phokoso lace limveka pa Nyanja Yofiira.

22 Taonani, adzafika nadzauluka ngati ciombankhanga, adzatambasulira Boma mapiko ace, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Edomu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.

Citsutso ca Damasiko

23 Za Damasiko. Hamati ndi Aripadi ali ndi manyazi, cifukwa anamva malodza, asungunuka kunyanja, adera nkhawa osatha kukhala cete.

24 Damasiko walefuka, atembenukira kuti athawe, kunthunthumira kwamgwira; zobvuta ndi kulira zamgwira iye, ngati mkazi alimkudwala.

25 Alekeranji kusiya mudzi wa cilemekezo, mudzi wa cikondwero canga?

26 Cifukwa cace anyamata ace adzagwa m'miseu yace, ndipo anthu onse a nkhondo adzatontholetsedwa tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu.

27 Ndipo Ine ndidzayatsa moto m'khoma la Damasiko, udzathetsa zinyumba za Beni-Hadadi.

Citsutso ca Kedara, Hazori ndi Elamu

28 Za Kedara, ndi za maufumu a Hazori, amene anawakantha Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo.Yehova atero: Ukani, kwerani ku Kedara, funkhani ana a kum'mawa.

29 Mahema ao ndi zoweta zao adzazilanda, adzadzitengera nsaru zocingira zao, ndi katundu wao yense, ndi ngamila zao; ndipo adzapfuulira iwo, Mantha ponse ponse.

30 Thawani inu, yendani kutari, khalani mwakuya, Inu okhala m'Hazori, ati Yehova; pakuti Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anapangira uphungu pa inu, nakulingalirirani.

31 Nyamukani, kwererani mtundu wokhala ndi mtendere, wokhala osadera nkhawa, ati Yehova, amene alibe zitseko ndi mipiringidzo, okhala pa okha.

32 Ndipo ngamila zao zidzakhala zofunkha, ndi unyinji wa ng'ombe zao udzakhala wolanda; ndipo ndidzabalalitsira ku mphepo zonse iwo amene ameta m'mbali mwa tsitsi lao; ndipo ndidzatenga tsoka lao ku mbali zao zonse, ati Yehova.

33 Ndipo Hazori adzakhala mokhalamo ankhandwe, bwinja lacikhalire; simudzakhalamo munthu, simudzagonamo mwana wa munthu.

34 Mau a Yehova amene anafika kwa Yeremiya mneneri, onena za Elamu poyamba kulamulira Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti,

35 Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatyola uta wa Elamu, ndiwo mtima wa mphamvu yao.

36 Pa Elamu ndidzatengera mphepo zinai ku mbali zinai za mlengalenga, ndidzamwaza iwo ku mphepo zonsezo; ndipo sikudzakhala mtundu kumene opitikitsidwa a Elamu sadzafikako.

37 Ndipo ndidzacititsa Elamu mantha pamaso pa amaliwongo ao, ndi pamaso pa iwo ofuna moyo wao; ndipo ndidzatengera coipa pa iwo, mkwiyo wanga waukali, ati Yehova; ndipo ndidzatumiza lupanga liwalondole, mpaka nditawatha;

38 ndipo ndidzaika mpando wacifumu wanga m'Elamu, ndipo ndidzaononga pamenepo mfumu ndi akulu, ati Yehova.

39 Koma padzaoneka masiku akutsiriza, kuti ndidzabwezanso undende wa Elamu, ati Yehova.