1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babulo, ndi nkhondo yace yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wace, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi midzi yace yonse, akuti:
2 Yehova Mulungu wa Israyeli atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la mfumu ya ku Babulo, ndipo adzautentha ndi moto;
3 ndipo iwe sudzapulumuka m'dzanja lace, koma udzagwiridwadi, nudzaperekedwa m'dzanja lace; ndipo maso ako adzaanana nao a mfumu ya ku Babulo, ndipo iye adzanena nawe pakamwa ndi pakamwa, ndipo udzanka ku Babulo.
4 Koma tamva mau a Yehova, iwe Zedekiya mfumu ya Yuda; Yehova atero za iwe, Sudzafa ndi lupanga;
5 udzafa ndi mtendere; ndipo adzawambika iwe monga anawambika makolo ako, mafumu akale usanakhale iwe; ndipo adzakulirira iwe, kuti, Kalanga ine ambuye! pakuti ndanena mau, ati Yehova.
6 Ndipo Yeremiya mneneri ananena mau onsewa kwa Zedekiya mfumu ya Yuda m'Yerusalemu,
7 pamene nkhondo ya mfumu ya ku Babulo inamenyana ndi Yerualemu, ndi midzi yonse ya Yuda imene inatsala, ndi Lakisi ndi Azeka; pakuti midzi ya Yuda yamalinga yotsala ndi imeneyi.
8 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, atapangana Zedekiya pangano ndi anthu onse amene anali pa Yerusalemu, kuti awalalikire iwo ufulu;
9 kuti yense ammasule kapolo wace wamwamuna, ndi wamkazi, pokhala iye Mhebri wamwamuna kapena wamkazi, kuti yense asayese Myuda mnzace kapolo wace;
10 ndipo akuru onse ndi anthu onse anamvera, amene anapangana mapangano, akuti yense ammasule kapolo wace wamwamuna, kapena wamkazi osawayesanso akapolo; iwo anamvera nawamasula;
11 koma pambuyo pace anabwerera, nabweza akapolo ace amuna ndi akazi, amene anawamasula, nawagonjetsanso akhale akapolo amuna ndi akazi;
12 cifukwa cace mau a Yehova anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,
13 Yehova Mulungu wa Israyeli atero: Ndinapangana mapangano ndi makolo anu tsiku lija ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, kuturuka m'nyumba ya ukapolo, kuti,
14 Zitapita zaka zisanu ndi ziwiri mudzaleka amuke yense mbale wace amene ali Mhebri, amene anagulidwa ndi inu, amene anakutumikirani inu zaka zisanu ndi cimodzi, mudzammasule akucokereni; koma makolo anu sanandimvera Ine, sanandichera Ine khutu,
15 Ndipo mwabwerera inu tsopano, ndi kucita cimene ciri colungama pamaso panga, pakulalikira ufulu yense kwa mnzace; ndipo munapangana pangano pamaso panga m'nyumba imene ichedwa dzina langa;
16 koma mwabwerera ndi kuipitsa dzina langa, ndi kubwezera m'ukapolo yense kapolo wace wamwamuna, ndi wamkazi, amene munammasula akacite zao, ndipo munawagonjetsa, akhale akapolo anu amuna ndi akazi.
17 Cifukwa cace Yehova atero: Simunandimvera Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wace, ndi munthu yense kwa mnzace; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kucaola, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.
18 Ndipo ndidzapereka anthu akulakwira pangano langa, amene sanacita mau a pangano limene anapangana pamaso panga, muja anadula pakati mwana wa ng'ombe ndi kupita pakati pa mbali zace;
19 akulu a Yuda, ndi akulu a Yerusalemu, adindo, ndi ansembe, ndi anthu onse a m'dziko, amene anapita pakati pa mbali za mwana wa ng'ombe;
20 ndidzapereka iwo m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la iwo akufuna moyo wao; ndipo mitembo yao idzakhala cakudya ca mbalame za mlengalenga, ndi ca zirombo za pa dziko lapansi.
21 Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda ndi akulu ace ndidzawapereka m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la akufuna moyo wao, ndi m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babulo, imene yakucokerani.
22 Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo ku mudzi uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.