Yeremiya 48 BL92

Citsutso ca Moabu

1 Za Moabu Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Tsoka Nebo! pakuti wapasuka; Kiriyataimu wacitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lacitidwa manyazi lapasudwa.

2 Palibenso kutamanda Moabu; m'Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu waanthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.

3 Mau amveka kucokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukuru!

4 Moabu waonongedwa; ang'ono ace amveketsa kulira.

5 Pakuti adzakwera pa cikweza ca Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa citsiko ca Horonaimu amva kulira kowawa kwa cionongeko.

6 Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amarisece m'cipululu,

7 Pakuti, cifukwa wakhulupirira nchito zanu ndi cuma canu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ace ndi akuru ace pamodzi.

8 Ndipo wakufunkha adzafikira pa midzi yonse, sudzapulumuka mudzi uli wonse; cigwa comwe cidzasakazidwa, ndipo cidikha cidzaonongedwa; monga wanena Yehova.

9 Patsani Moabu mapiko, kuti athawe apulumuke; midzi yace ikhale bwinja, lopanda wokhalamo.

10 Atembereredwe iye amene agwira nchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lace kumwazi.

11 Moabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wace, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; cifukwa cace makoleredwe ace alimobe mwa iye, pfungo lace silinasinthika.

12 Cifukwa cace, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zace, nadzaswa zipanda zao.

13 Ndipo Moabu adzacita manyazi cifukwa ca Kemosi, monga nyumba ya Israyeli inacita manyazi cifukwa ca Beteli amene anamkhulupirira,

14 Muti bwanji, Tiri amphamvu, olimba mtima ankhondo?

15 Moabu wapasuka, akwera kulowa m'midzi yace, ndi anyamata ace osankhika atsikira kukaphedwa, ati Mfumu, dzina lace ndiye Yehova wa makamu.

16 Tsoka la Moabu layandikira kudza, nsautso yace ifulumiratu.

17 Inu nonse akumzungulira, mumcitire iye cisoni, inu nonse akudziwa dzina lace; muti, Cibonga colimba catyokatu, ndodo yokoma!

18 Iwe mwana wamkazi wokhala m'Diboni, utsike pa ulemerero wako, nukhale ndi ludzu; pakuti wakufunkha Moabu wakukwerera, iwe waononga malinga ako.

19 Iwe wokhala m'Aroeri, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Cacitidwa ciani?

20 Moabu wacitidwa manyazi, pakuti watyoka; kuwa nulire, nunene m'Arinoni, kuti Moabu wapasuka.

21 Ciweruzo cafika pa dziko lacidikha; pa Holoni, ndi pa Yaza, ndi pa Mefati;

22 ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Beti-Dibilataimu;

23 ndi pa Kiriataimu, ndi pa Beti-Gamuli, ndi pa Beti-Meoni;

24 ndi pa Kerioti, ndi pa Bozira, ndi pa midzi yonse ya dziko la Moabu, yakutari kapena yakufupi.

25 Nyanga ya Moabu yaduka, ndipo watyoka mkono wace, ati Yehova.

26 Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Moabu yemwe adzabvimvinika m'kusanza kwace, ndipo iye adzasekedwanso.

27 Kodi sunaseka Israyeli? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu.

28 Inu okhala m'Moabu, siyani midzi, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja cisanja cace pambali pakamwa pa dzenje.

29 Ife tamva kudzikuza kwa Moabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwace, ndi kunyada kwace, ndi kudzitama kwace, ndi kudzikuza kwa mtima wace.

30 Ine ndidziwa mkwiyo wace, ati Yehova, kuti uli cabe; zonyenga zace sizinacita kanthu.

31 Cifukwa cace ndidzakuwira Moabu; inde, ndidzapfuulira Moabu yense, adzalirira anthu a ku Kirere.

32 Iwe mpesa wa Sibima; ndidzakulirira iwe ndi kulira kopambana kulira kwa Yazeri, nthambi zako zinapitirira nyanja, zinafikira ku nyanja ya Yazeri; wakufunkha wagwera zipatso zako za mpakasa ndi mphesa zako.

33 Ndipo kusekera ndi kukondwa kwacotsedwa, ku munda wobala ndi ku dziko la Moabu; ndipo ndaletsa vinyo pa zoponderamo; sadzaponda ndi kupfuula; kupfuula sikudzakhala kupfuula.

34 Kuyambira kupfuula kwa Hesiboni mpaka ku Eleale, mpaka ku Yahazi anakweza mau, kuyambira pa Zoari mpaka ku Horonaimu, ku Egilati-Selisiya; pakuti pa madzi a ku Nimurimu komwe padzakhala mabwinja.

35 Ndiponso ndidzaletsa m'Moabu, ati Yehova, iye amene apereka nsembe pamsanje, ndi iye amene afukizira milungu yace.

36 Cifukwa cace mtima wanga umlima Moabu monga zitolilo, ndipo mtima wanga uwalirira anthu a Kireresi monga zitolilo, cifukwa cace zakucuruka zace adadzionera zatayika.

37 Pakuti mitu yonse iri yadazi, ndipo ndebvu ziri zosengedwa; pa manja onse pali pocekedwa-cekedwa, ndi pacuuno ciguduli.

38 Pamwamba pa macindwi a Moabu ndi m'miseu mwace muli kulira monse monse; pakuti ndaswa Moabu monga mbiya m'mene mulibe cikondwero, ati Yehova.

39 Yasweka bwanji! Akuwa bwanji Moabu! Wapotoloka bwanji ndi manyazi! Comweco Moabu adzakhala coseketsa ndi coopsera onse omzungulira iye.

40 Pakuti Yehova atero: Taonani, adzauluka ngati ciombankhanga, adzamtambasulira Moabu mapiko ace.

41 Keroti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Moabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.

42 Ndipo Moabu adzaonongeka asakhalenso mtundu wa anthu, cifukwa anadzikuzira yekha pa Yehova.

43 Mantha, ndi dzenje, ndi khwekhwe, ziri pa iwe, wokhala m'Moabu, ati Yehova.

44 Ndipo iye wakuthawa cifukwa ca mantha adzagwa m'dzenje; ndi iye amene aturuka m'dzenje adzagwidwa m'khwekhwe; pakuti ndidzatengera pa iye, pa Moabu, caka ca kulangidwa kwao, ati Yehova.

45 Iwo amene anathawa aima opanda mphamvu pansi pa mthunzi wa Hesiboni; pakuti moto waturuka m'Hesiboni, ndi malawi a moto m'kati mwa Sihoni, nadya ngondya ya Moabu, ndi pakati pamtu pa ana a phokoso,

46 Tsoka iwe, Moabu! anthu a Kemosi athedwa; pakuti ana ako amuna atengedwa ndende, ndi ana ako akazi atengedwa ndende.

47 Koma ndidzabwezanso undende wa Moabu masiku akumariza, ati Yehova. Ziweruzo za Moabu ndi zomwezi.