1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova caka cakhumi ca Zedekiya mfumu ya Yuda, cimene cinali caka cakhumi ndi cisanu ndi citatu ca Nebukadirezara.
2 Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babulo inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali ku nyumba ya mfumu ya Yuda.
3 Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Cifukwa canji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mudzi uwu m'dzanja la mfumu ya Babulo, ndipo iye adzaulanda,
4 ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Akasidi, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babulo, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;
5 ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babulo, ndipo adzakhala komwe kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Akasidi, simudzapindula konse?
6 Ndipo Yeremiya anati, Mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,
7 Taonani, Hanameli mwana wa Salumu mbale wa atate wako adzadza kwa iwe, kuti, Ugule munda wanga uli ku Anatoti; pakuti mphamvu yakuombola ndi yako kuugula.
8 Ndipo Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga anadza kwa ine m'bwalo la kaidi monga mwa mau a Yehova, nati kwa ine, Gulatu munda wanga, wa ku Anatoti, m'dziko la Benjamini; pakuti mphamvu yakulowa ndi yakuombola ndi yako; udzigulire wekha. Pamenepo ndinadziwa kuti awa ndi mau a Yehova.
9 Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanameli mwana wa cibale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekele khumi ndi asanu ndi awiri a siliva.
10 Ndipo ndinalemba cikalataco, ndicisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m'miyeso.
11 Ndipo ndinatenga kalata wogulira, wina wosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi wina wobvundukuka;
12 ndipo ndinapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseya, pamaso pa Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata wogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la kaidi.
13 Ndipo ndinauza Baruki pamaso pao, kuti,
14 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero; Tenga akalata awa, kalata uyu wogulira, wosindikizidwa, ndi kalata uyu wobvundukuka, nuwaike m'mbiya yadothi; kuti akhale masiku ambiri.
15 Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero: Nyumba ndi minda ndi minda yamphesa idzagulidwanso m'dziko muno.
16 Ndipo nditapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, ndinapemphera kwa Yehova, kuti,
17 Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikuru ndi mkono wanu wotambasuka; palibe cokulakani Inu;
18 a amene mucitira cifundo anthu zikwi; nimubwezera mphulupulu ya atate m'cifuwa ca ana ao a pambuyo pao, dzina lace ndi Mulungu wamkuru, wamphamvu, Yehova wa makamu;
19 wamkuru, m'upo, wamphamvu m'nchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa cipatso ca macitidwe ace;
20 amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m'dziko la Aigupto, mpaka lero lomwe, m'Israyeli ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;
21 ndipo munaturutsa anthu anu Israyeli m'dziko la Aigupto ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri;
22 ndipo munawapatsa iwo dziko ili, limene munalumbirira makolo ao kuti mudzawapatsa, dziko moyenda mkaka ndi uci;
23 ndipo analowa, nakhalamo; koma sa namvera mau anu, sanayenda m'cilamulo canu; sanacita kanthu ka zonse zimene munawauza acite; cifukwa cace mwafikitsa pa iwo coipa conseci;
24 taonani mitumbira, yafika kumudzi kuugwira, ndipo mudzi uperekedwa m'dzanja la, Akasidi olimbana nao, cifukwa ca lupanga, ndi cifukwa ca njala, ndi cifukwa ca caola; ndipo cimene munacinena caoneka; ndipo, taonani, muciona.
25 Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mudzi waperekedwa m'manja a Akasidi.
26 Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,
27 Taona, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu lonse; kodi kuli kanthu kondilaka Ine?
28 Cifukwa cace Yehova atero: Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la Akasidi, m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, ndipo iye adzaulanda,
29 ndipo Akasidi, olimbana ndi mudzi uwu, adzafika nadzayatsa mudziwu, nadzautentha, pamodzi ndi nyumba, zimene anafukizira Baala, pa macitidwe ao, ndi kutsanulirira milungu yina nsembe zothira, kuti autse mkwiyo wanga.
30 Pakuti ana a Israyeli ndi ana a Yuda anacita zoipa zokha zokha pamaso panga ciyambire ubwana wao, pakuti ana a Israyeli anandiputa Ine kokha kokha ndi nchito ya manja ao, ati Yehova.
31 Pakuti mudzi uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiucotse pamaso panga;
32 cifukwa ca zoipa zonse za ana a Israyeli ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu.
33 Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m'mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvera kulangizidwa.
34 Koma anaika zonyansa zao m'nyumba yochedwa dzina langa, kuti aidetse.
35 Ndipo anamanga misanje ya Baala, iri m'cigwaca mwana wace wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao amuna ndi akazi cifukwa ca Moleki; cimene sindinauza, cimene sicinalowa m'mtima mwanga, kuti acite conyansa ici, cocimwitsa Yuda.
36 Cifukwa cace tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, za mudzi umene, munena inu, waperekedwa m'dzanja la mfumu ya Babulo ndi lupanga, ndi njala, ndi caola:
37 Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapitikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukuru, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,
38 ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao;
39 ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwacitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;
40 ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawacokera kuleka kuwacitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandicokere.
41 Inde, ndidzasekerera iwo kuwacitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.
42 Pakuti atero Yehova: Monga ndatengera anthu awa coipa conseci, comweco ndidzatengera iwo zabwino zonse ndawalonieza.
43 Ndipo minda idzagulidwa m'dziko lino, limene muti, Ndilo bwinja, lopanda munthu kapena nyama; loperekedwa m'dzanja la Akasidi.
44 Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera akalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'midzi ya Yuda, ndi m'midzi ya kumtunda, ndi m'midzi ya kucidikha, ndi m'midzi ya ku Mwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.