1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,
2 Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, kuti, Lemba m'buku mau onse amene ndanena kwa iwe.
3 Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisrayeli ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera ku dziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo.
4 Awa ndi mau ananena Yehova za Israyeli ndi Yuda.
5 Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere.
6 Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; cifukwa canji ndiona mwamuna ndi manja ace pa cuuno cace, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?
7 Kalanga ine! pakuti nlalikuru tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.
8 Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzatyola gori lace pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;
9 koma adzamtumikira Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, imene ndidzawaukitsira.
10 Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israyeli; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutari, ndi mbeu zako ku dziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala cete, palibe amene adzamuopsya.
11 Pakuti Ine ndiri ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi ciweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosaparamula.
12 Pakuti atero Yehova, Kulaswa kwako kuti kosapoleka ndi bala lako liri lowawa.
13 Palibe amene adzanenera mlandu wako, ulibe mankhwala akumanga nao bala lako.
14 Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; cifukwa ca mphulupulu yako yaikuru, cifukwa zocimwa zako zinacuruka.
15 Cifukwa canji ulilira bala lako? kuphwetekwa kwako kuli kosapoleka; cifukwa ca mphulupulu yako yaikuru, cifukwa zocimwa zako zinacuruka, ndakucitira iwe izi.
16 Cifukwa cace iwo akulusira iwe adzalusidwanso; ndi adani ako onse, adzanka kuundende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala cofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao.
17 Pakuti ndidzakubwezera iwe moyo, ndipo ndidzapoletsa mabala ako, ati Yehova; cifukwa anacha iwe wopitikitsidwa, nati, Ndiye Ziyoni, amene kulibe munthu amfuna.
18 Atero Yehova: Taonani, ndidzabwezanso undende wa mahema a Yakobo, ndipo ndidzacitira cifundo zokhalamo zace, ndipo mudzi udzamangidwa pamuunda pace, ndi cinyumba cidzakhala momwe.
19 Ndipo padzaturuka pa izo mayamikiro ndi mau a iwo okondwerera; ndipo ndidzacurukitsa iwo, sadzakhala owerengeka; ndidzawacitiranso ulemu, sadzacepa.
20 Ana aonso adzakhala monga kale, ndipo msonkhano wao udzakhazikika pamaso panga, ndipo ndidzalanga onse amene akupsinja iwo.
21 Ndipo mkuru wao adzakhala mwa iwo, ndi wolamulira wao adzaturuka pakati pao; ndipo ndidzamyandikitsa iye, ndipo adzayandikira kwa Ine, pakuti iye wolimba mtima kuyandikira kwa Ine ndani? ati Yehova.
22 Ndipo inu mudzakhala anthu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu.
23 Taonani, cimphepo ca Yehova, kupsya mtima kwace, caturuka, cimphepo cakukokolola: cidzagwa pamtu pa oipa.
24 Mkwiyo waukali wa Yehova sudzabwerera, mpaka wacita, mpaka watha zomwe afuna kucita m'mtima mwace: masiku akumariza mudzacizindikira.