Yeremiya 2 BL92

Yehova adzudzula anthu a lsrayeli

1 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, nati,

2 Pita nupfuule n'makutu a Yerusalemu, kuti, Yehova atero, Ndikumbukira za iwe kukoma mtima kwa ubwana wako, cikondi ca matomedwe ako; muja unanditsata m'cipululu m'dziko losabzya lamo.

3 Israyeli anali wopatulikira Yehova, zipatso zoundukula za zopindula zace; onse amene adzamudya iye adzayesedwa oparamula; coipa cidzawagwera, ati Yehova.

4 Tamvani mau a Yehova, iwe nyumba ya Yakobo, ndi inu mabanja onse a nyumba ya Israyeli;

5 atero Yehova, Atate anu apeza cosalungama canji mwa Ine, kuti andicokera kunka kutari, natsata zacabe, nasanduka acabe?

6 Osati, Ali kuti Yehova amene anatikweza kucokera ku dziko la Aigupto, natitsogolera m'cipululu, m'dziko loti se ndi la maenje, m'dziko la cirala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitamo anthu, losamangamo anthu?

7 Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zace, ndi zabwino zace; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa colandira canga conyansa.

8 Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.

9 Cifukwa cace ndidzatsutsananso nanu, ati Yehova, ndi ana a ana anu ndidzatsutsana nao.

10 Pakuti pitani ku zisumbu za Kitimu nimuone; tumizani ku Kedara nimulingalire bwino; nimuone ngati cinalipo cotere.

11 Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siiri milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi cosapindula.

12 Muzizwe pamenepo, miyamba inu, muope kwambiri, mukhale ouma, ati Yehova.

13 Pakuti anthu anga anacita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi.

14 Kodi Israyeli ndi mtumiki? kodi ndiye kapolo wobadwa m'nyumba? afunkhidwa bwanji?

15 Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lace, midzi yace yatenthedwa, mulibenso wokhalamo.

16 Ananso a Nofi ndi a Tahapanesi, anaswa pakati pamtu pako.

17 Kodi sunadzicitira ici iwe wekha popeza unasiya Yehova Mulungu wako, pamene anatsogolera iwe panjira?

18 Tsopano uli naco ciani m'njira ya ku Aigupto, kumwa madzi a Sihori? uli naco ciani m'njira ya ku Asuri, kumwa madzi a m'Nyanja?

19 Coipa cako cidzai kulanga iwe, mabwerero ako adzakudzudzula iwe; dziwa, nuone, kuti ici ndi coipa ndi cowawa, kuti wasiya Yehova Mulungu wako, ndi kuti kundiopa Ine sikuli mwa iwe, ati Yehova Mulungu wa makamu.

20 Pakuti kale lomwe ndinatyola gori lako, ndi kudula zomangira zako; ndipo unati, Sindidzakutumikirani, pakuti pa zitunda zonse zazitari, ndi patsinde pa mitengo yonse yaiwisi unawerama, ndi kucita dama.

21 Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pace, ya mpesa wacilendo?

22 Pakuti ngakhale usamba ndi soda, ndi kudzitengera sopo wambiri, mphulupulu zako zidziwika pamaso panga, ati Yehova Mulungu.

23 Bwanji uti, Sindinaipitsidwa, sindinatsata Abaala? Ona njira yako m'cigwa, dziwa cimene wacicita; ndiwe ngamila yothamanga yoyenda m'njira zace;

24 mbidzi yozolowera m'cipululu, yopumira mphepo pakufuna pace; pokomana nayo ndani adzaibweza? onse amene aifuna sadzadzilemetsa; adzaipeza m'mwezi wace.

25 Kaniza phazi lako lisakhale losabvala nsapato, ndi m'mero mwako musakhale ndi ludzu; koma unati, Palibe ciyembekezo, iai; pakuti ndakonda alendo, ndipo ndidzatsata pambuyo pao.

26 Monga mbala iri ndi manyazi pamene igwidwa, comweco nyumba ya Israyeli iri ndi manyazi; iwo, mafumu ao, akuru ao, ansembe ao, ndi aneneri ao;

27 amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kubvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.

28 Koma iri kuti milungu yako imene wadzipangira? Iuke, ikupulumutse iwe m'nthawi ya kubvutidwa kwako; pakuti milungu yako ilingana ndi kucuruka kwa midzi yako, Yuda iwe.

29 Cifukwa canji mudzatsutsana ndi Ine nonse? mwandilakwira Ine, ati Yehova.

30 Ndapanda ana anu mwacabe; sanamvera kulanga; lupanga lanu ladya aneneri anu, monga mkango wakuononga.

31 Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israyeli cipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Cifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?

32 Kodi angathe namwali kuiwala zokometsera zace, kapena mkwatibwi zobvala zace? koma anthu anga andiiwala Ine masiku osawerengeka.

33 Kodi sukonzadi njira yako kufunafuna cilakolako? cifukwa cace waphunzitsa akazi oipa njira zako.

34 Ndiponso m'nsaru zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osacimwa; sunawapeza pakuboola, koma ponsepo.

35 Koma unati, Ndiri wosacimwa ndithu; mkwiyo wace wacoka pa ine. Taona, ndidzakuweruza iwe, cifukwa uti, Sindinacimwa.

36 Bwanji uyendayenda kwambiri ndi kusintha njira yako? udzacitanso manyazi ndi Aigupto monga unacita manyazi ndi Asuri.

37 Koma udzaturuka kwa iyenso, manja ako pamtu pako; pakuti Yehova wakana zokhulupirira zako, ndipo sudzapindula m'menemo.