Yeremiya 3 BL92

1 Amati, Ngati mwamuna acotsa mkazi wace, ndipo amcokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wacita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.

2 Kwezera maso ako ku mapiri oti se, nuone: sanagona ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga M-arabu m'cipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako.

3 Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi.

4 Kodi kuyambira tsopano sudzapfuulira kwa Ine, Atate wanga, wotsogolera ubwana wanga ndinu?

5 Kodi adzasunga mkwiyo wace ku nthawi zonse? Kodi adzakudikira mpaka cimariziro? Taona, wanena ndi kucita zoipa monga unatero.

Abwere kwa Yehova anthu olowererawo

6 Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona cimene wacicita Israyeli, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri atari onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kucita dama pamenepo.

7 Ndipo ndinati atacita zimenezo zonse, Adzabwera kwa Ine; koma sanabwere, ndipo mphwace wonyenga, Yuda, anaona.

8 Ndipo ndinaona, kuti, ndingakhale ndikamcotsa Israyeli wobwerera m'mbuyo, ndi kumpatsa kalata wacilekaniro cifukwa ca kucita cigololo iye, mphwace Yuda wonyenga sanaope, koma iye yemwe ananka nacita dama.

9 Ndipo kunali kuti mbiri ya dama lace inaipitsa dziko, ndipo anacita cigololo ndi miyala ndi mitengo.

10 Ndipo zingakhale zonsezi mphwace wonyenga sanabwera kwa Ine ndi mtima wace wonse, koma monama, ati Yehova.

11 Ndipo Yehova anati kwa ine, Israyeli wobwerera anadzionetsa wolungama kopambana ndi Yuda wonyenga,

12 Pita; nulalikire mau awa kuyang'ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israyeli wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang'anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndiri wacifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya ku nthawi zonse.

13 Koma bvomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvera mau anga, ati Yehova.

14 Bwerani, ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye wanu; ndipo ndidzakutengani inu mmodzi mmodzi wa pa mudzi uli wonse, ndi awiri awiri a pa banja liri lonse, ndi kukutengerani ku Ziyoni;

15 ndipo ndidzakupatsani inu abusa monga mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha.

16 Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kucuruka m'dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse, Likasa la cipangano ca Yehova; silidzalowa m'mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzacitanso konse.

17 Pa nthawi yomweyo adzacha Yerusalemu mpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m'kuumirira kwa mtima wao woipa.

18 Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderana ndi nyumba ya Israyeli, ndipo adzaturuka pamodzi ku dziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo.

19 Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, colowa cabwino ca makamu a mitundu ya anthu? ndipo ndinati mudzandicha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.

20 Ndithu monga mkazi acokera mwamuna wace monyenga, comweco mwacita ndi Ine monyenga, inu nyumba ya Israyeli, ati Yehova.

21 Mau amveka pa mapiri oti se, kulira ndi kupempha kwa ana a Israyeli; pakuti anaipitsa njira yao, naiwala Yehova Mulungu wao.

22 Bwerani, ana inu obwerera, ndidzaciritsa mabwerero anu. Taonani, tadza kwa Inu; pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.

23 Ndithu akhulupirira mwacabe cithandizo ca kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli cipulumutso ca Israyeli,

24 Ndipo cocititsa manyazi cinathetsa nchito za atate athu kuyambira ubwana wathu; nkhosa zao ndi zoweta zao, ana ao amuna ndi akazi.

25 Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutipfunde ife; pakuti tamcimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvera mau a Yehova Mulunguwathu.