Yeremiya 38 BL92

Yeremiya aponyedwa m'dzenje muli thope

1 Ndipo Sefatiya mwana wa Matani ndi Gedaliya mwana wa Pusuri, ndi Yukali mwana wa Selemiya, ndi Pasuri mwana wa Malikiya, anamva mau amene Yeremiya ananena ndi anthu onse, kuti,

2 Yehova atero, Iye wakukhala m'mudziwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; koma iye wakuturukira kunka kwa Akasidi adzakhala ndi moyo, ndipo adzakhala nao moyo wace ngati cofunkha, nadzakhala ndi moyo.

3 Yehova atero, Mudziwu udzapatsidwatu m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babulo, ndipo adzaulanda.

4 Ndipo akuru anati kwa mfumu, Munthu uyu aphedwetu; cifukwa analopetsa manja a anthu a nkhondo otsala m'mudzi uno, ndi manja a anthu onse, pakunena kwa iwo mau otero; pakuti munthu uyu safuna mtendere wa anthu awa, koma nsautso yao.

5 Ndipo mfumu Zedekiya anati, Taonani, ali m'manja mwanu; pakuti mfumu singathe kucita kanthu kotsutsana nanu.

6 Ndipo anatenga Yeremiya, namponya iye m'dzenje la Malikiya mwana wace wa mfumu, limene linali m'bwalo la kaidi; ndipo anamtsitsa Yeremiya ndi zingwe, Koma m'dzenjemo munalibe madzi, koma thope; namira Yeremiya m'thopemo.

7 Ndipo pamene Ebedi-Meleki Mkusi, mdindo, anamva kuti anamuika Yeremiya m'dzenje; mfumu irikukhala pa cipata ca Benjamini;

8 Ebedi-Meleki anaturuka m'nyumba ya mfumu, nanena ndi mfumu, kuti,

9 Mbuyanga mfumu, anthu awa anacita zoipa m'zonse anacitira Yeremiya mneneri, amene anamponya m'dzenje; ndipo afuna kufa m'menemo cifukwa ca njala; pakuti mulibe cakudya cina m'mudzimu.

10 Ndipo mfumu inamuuza Ebedi-Meleki Mkusi, kuti, Tenga anthu makumi atatu, umkweze numturutse Yeremiya mneneri m'dzenjemo, asanafe.

11 Ndipo Ebedi-Meleki anatenga anthuwo, nalowa nao m'nyumba ya mfumu ya pansi pa nyumba ya cuma, natenga m'menemo nsaru zakale zotaya ndi zansanza zobvunda, nazitsitsira ndi zingwe kwa Yeremiya m'dzenjemo.

12 Ndipo Ebedi-Meleki Mkusi anati kwa Yeremiya, Kulungatu zingwe ndi nsaruzi zotaya zakale ndi zansanza ndi kuzikwapatira. Ndipo Yeremiya anacita comweco.

13 Ndipo anamkweza Yeremiya ndi zingwe, namturutsa m'dzenjemo; ndipo Yeremiya anakhalabe m'bwalo la kaidi.

14 Ndipo mfumu Zedekiya anatuma, natntenga Yeremiya mneneri nalowa naye m'khomo lacitatu la nyumba ya Yehova; ndipo mfumu inati kwa Yeremiya, Ndidzakufunsa iwe kanthu; usandibisire ine kanthu.

15 Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Ndikakufotokozerani, kodi simudzandipha ine? ndipo ndikakupangirani, simudzandimveta ine.

16 Ndipo Zedekiya analumbira m'tseri kwa Yeremiya, kuti, Pali Yehova, amene anatilengera ife moyo uno, sindidzakupha iwe sindidzakupereka iwe m'manja mwa anthu awa amene afuna moyo wako.

17 Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Ngati mudzaturukira kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, mudzakhala ndi moyo, ndipo mudziwu sudzatenthedwa ndi moto; ndipo mudzakhala ndi moyo ndi banja lanu;

18 koma ngati simudzaturukira kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, mudziwu udzaperekedwa m'dzanja la Akasidi, ndipo udzatenthedwa ndi moto, ndipo simudzapulumuka m'manja mwao.

19 Ndipo mfumu Zedekiya anati kwa Yeremiya, Ine ndiopa Ayuda amene anandipandukira ine kunka kwa Akasidi, angandipereke ine m'manja mwao, angandiseke.

20 Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, comweco kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.

21 Koma ngati mukana kuturuka, mau anandisonyeza Yehova ndi awa:

22 Taonani, akazi onse otsala m'nyumba ya mfumu ya Yuda adzaturutsidwa kunka kwa akuru a mfumu ya ku Babulo, ndipo akaziwo adzati, Oyanjana nanu anakunyengani, ndi kukuposani inu, mapazi anu amire m'thope, abwerera m'mbuyo.

23 Ndipo adzaturutsira Akasidi akazi anu onse, ndi ana anu, ndipo simudzapulumuka m'manja ao, koma mudzagwidwa ndi dzanja la mfumu ya ku Babulo; ndipo mudzatenthetsa mudziwu ndi moto.

24 Ndipo Zedekiya anati kwa Yeremiya, Anthu asadziwe mau amene, ndipo sudzafa.

25 Koma akamva akuru kuti ndalankhula ndi iwe, nakafika kwa iwe, ndi kuti kwa iwe, Utifotokozere ife comwe wanena kwa mfumu; osatibisira ici, ndipo sitidzakupha iwe; ndiponso zomwe mfumu inanena kwa iwe;

26 pamenepo uziti kwa iwo, Ndinagwa ndi pembedzero langa pamaso pa mfumu, kuti asandibwezerenso ku nyumba ya Yonatani ndifere komweko.

27 Ndipo akuru onse anadza kwa Yeremiya, namfunsa; ndipo iye ananena nao monga mwa mau onsewo anamuuza mfumu. Ndipo analeka kunena naye; pakuti sikunamveka mlandu.

28 Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi mpaka dzuwa lakugwidwa Yerusalemu. Ndipo anali komweko pogwidwa Yerusalemu.