1 Atero Yehova, Pita, nugule nsupa ya woumba, nutenge akuru a anthu, ndi akuru a ansembe;
2 nuturukire ku cigwa ca mwana wace wa Hinomu, cimene ciri pa khomo la cipata ca mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;
3 nuti, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzatengera malo ano coipa, cimene ali yense adzacimva, makutu ace adzacita woo.
4 Cifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano acilendo, nafukizira m'menemo milungu yina, imene sanaidziwa, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda: nadzaza malo ano ndi mwazi wa osacimwa;
5 namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, cimene sindinawauza, sindinacinena, sicinalowa m'mtima mwanga;
6 cifukwa cace, taonani, masiku adza, ati Yehova kuti pamalo pano sipadzachedwanso Tofeti, kapena Cigwa ca mwana wace wa Hinomu, koma Cigwa Cophera anthu.
7 Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi wa Yerusalemu m'malo ano; ndipo ndidzagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi pa dzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndidzapatsa ikhale cakudya ca mbalame za m'mlengalenga, ndi ca zirombo za dziko lapansi.
8 Ndipo ndidzayesa mudziwu codabwitsa, ndi cotsonyetsa; onse amene adzapitapo adzadabwa ndi kutsonya cifukwa ca zopanda pace zonse.
9 Ndipo ndidzadyetsa iwo mnofu wa ana ao amuna ndi akazi, ndipo adzadya yense mnofu wa mbale wace, m'nkhondo yozinga ndi m'kupsinjikako, kumene adani ao, ndi iwo akufuna moyo wao, adzapsinja iwo nako.
10 Pamenepo uziphwanya nsupa pamaso pa anthu otsagana ndi iwe,
11 nuziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Comweco ndidzaphwanya anthu awa ndi mudzi uwu, monga aphwanya mbiya ya woumba, imene sangathe kulumbanso, ndipo adzaika maliro m'Tofeti, mpaka mulibe malo akuikamo.
12 Ndidzatero ndi malo ano, ati Yehova, ndi okhalamo, kusanduliza mudzi uwu ngati Tofeti;
13 ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu yina nsembe zothira.
14 Pamenepo Yeremiya anadza kucokera ku Tofeti, kumene Yehova anamtuma iye kuti anenere; ndipo anaima m'bwalo la nyumba ya Yehova, nati kwa anthu onse:
15 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzatengera mudzi uwu ndi midzi yace yonse coipa conse cimene ndaunenera; cifukwa anaumitsa khosi lao, kuti asamve mau anga.