1 Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, mitanga iwiri ya nkhuyu yoikidwa pakhomo pa Kacisi wa Yehova; Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo atacotsa am'nsinga Yekoniya mwana wace wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akuru a Yuda, ndi amisiri ndi acipala, kuwacotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babulo.
2 Mtanga umodzi unali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kuca; ndipo mtanga umodzi unali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.
3 Ndipo Yehova anati kwa ine, Kodi uona ciani, Yeremiya? Ndipo ndinati, Nkhuyu, nkhuyu zabwino, nzabwino ndithu; zoipazo nzoipa ndithu, zosadyeka poti nzoipa.
4 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,
5 Cifukwa Yehova, Mulungu wa Israyeli, atero, Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira am'nsinga a Yuda, amene ndawacotsera m'malo muno kunka ku dziko la Akasidi, kuwacitira bwino.
6 Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwacitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso ku dziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzyala, osawazula iwo.
7 Ndipo ndidzapatsa iwo mtima wakundidziwa, kuti ndine Yehova; nadzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao; pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao.
8 Ndipo, monga nkhuyu zoipa, zosadyeka, poti nzoipa; ntheradi atero Yehova, Comweco ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi akulu ace, ndi otsala a m'Yerusalemu, amene atsala m'dziko ili, ndi amene akhala m'dziko la Aigupto.
9 Ndipo ndidzawapatsa akhale coopsetsa coipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale citonzo ndi nkhani ndi coseketsa, ndi citemberero, monse m'mene ndidzawapitikitsiramo.
10 Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi caola mwa iwo, mpaka athedwa m'dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo ao.