Yeremiya 17 BL92

Cimo la Yuda ndi losafafanizika

1 Cimo la Yuda lalembedwa ndi peni lacitsulo, ndi nsonga ya diamondi; lalembedwa pa colembapo ca m'mtima mwao, ndi pa nyanga za maguwa a nsembe anu.

2 Pokumbukira ana ao maguwa a nsembe ao ndi zoimiritsa zao ku mitengo yaiwisi ya pa zitunda zazitari.

3 Iwe phiri langa la m'munda, ndidzapereka cuma cako ndi zosungidwa zako zikafunkhidwe, ndi misanje yako, cifukwa ca cimo, m'malire ako onse.

4 Iwe, iwe wekha, udzaleka pa colowa cako cimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha ku nthawi zamuyaya.

Anthu azikhulupirira Yehova yekha

5 Atero Yehova: Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wanyama, nucoka kwa Yehova mtima wace.

6 Ndipo adzakhala ngati tsanya la m'cipululu, ndipo saona pamene cifika cabwino; koma adzakhala m'malo oumitsa m'cipululu, dziko lacikungu lopanda anthu.

7 Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene cikhulupiriro cace ndi Yehova.

8 Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuti madzi, wotambalitsa mizu yace pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lace likhala laliwisi; ndipo subvutika cakaca cirala, suleka kubala zipatso.

9 Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosaciritsika, ndani angathe kuudziwa?

10 Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa imso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zace, monga zipatso za nchito zace.

11 Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikira, momwemo iye amene asonkhanitsa cuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ace cidzamsiya iye, ndipo pa citsirizo adzakhala wopusa.

12 Malo opatulika athu ndiwo mpando wacifumu wa ulemerero, wokhazikika pamsanje ciyambire.

13 Inu Yehova, ciyembekezo ca Israyeli, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondicokera Ine adzalembedwa m'dothi, cifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.

14 Mundiciritse ine, Yehova, ndipo ndidzaciritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti cilemekezo canga ndinu.

15 Taonani, ati kwa ine, Mau a Yehova ali kuti? adze tsopano.

16 Koma ine, pokhala mbusa sindinafulumira kucokerako kuti ndikutsateni Inu; sindinakhumba tsiku la tsoka; Inu mudziwa, cimene cinaturuka pa milomo yanga cinali pamaso panu.

17 Musakhale wondiopsetsa ine; ndinu pothawira panga tsiku la coipa.

18 Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la coipa, muwaononge ndi cionongeko cowirikiza.

Za kusunga dzuwa la Sabata

19 Yehova anatero kwa ine: Pita, nuime m'cipata ca ana a anthu, m'mene alowamo mafumu a Yuda, ndi m'mene aturukamo, ndi m'zipata zonse za Yerusalemu;

20 ndipo uziti kwa iwo, Tamvani mau a Yehova, inu mafumu a Yuda, ndi Ayuda onse, ndi onse okhala m'Yerusalemu, amene alowa pa zipatazi;

21 atero Yehova: Tadziyang'anirani nokha, musanyamule katundu tsiku la Sabata, musalowe naye pa zipata za Yerusalemu;

22 musaturutse katundu m'nyumba zanu tsiku la Sabata, musagwire nchito iri onse; koma mupatule tsiku la Sabata, monga ndinauza makolo anu;

23 koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma anaumitsa khosi lao, kuti asamve, asalandire langizo.

24 Ndipo padzakhala, ngati mu ndimveretsa Ine, ati Yehova, kuti musalowetse katundu pa zipata za mudzi uwu tsiku la Sabata, koma mupatule tsiku la Sabata, osagwira nchito m'menemo;

25 pamenepo padzalowa pa zipata za mudzi uwu mafumu ndi akuru okhala pa mpando wacifumu wa Davide, okwera pa magareta ndi akavalo, iwo, ndi akuru ao, anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu; ndipo mudzi uwu udzakhala ku nthawi zamuyaya.

26 Ndipo adzacokera ku midzi ya Yuda, ndi ku malo akuzungulira Yerusalemu, ndi ku dziko la Benjamini, ndi kucidikha, ndi kumapiri, ndi ku Mwela, ndi kudza nazo nsembe zopsereza, ndi nsembe zophera, ndi nsembe zaufa, ndi zonunkhira, ndi kudza nazo zamiyamikiro, ku nyumba ya Yehova.

27 Koma ngati simudzamvera Ine kulipatula tsiku la Sabata, kusanyamula katundu ndi kulowa pa zipata za Yerusalemu tsiku la Sabata; pamenepo ndidzayatsa moto m'zipata zacezo, ndipo udzatha zinyumba za Yerusalemu, osazimidwanso.