1 Ndiponso mau a Mulungu anadza kwa ine, kuti,
2 Usatenge mkazi, usakhale ndi ana amuna ndi akazi m'malo muno.
3 Pakuti Yehova atero za ana amuna ndi za ana akazi akubadwa m'malo muno, ndi za amai anawabala iwo, ndi za atate ao anawabala iwo m'dziko muno:
4 Adzafa ndi imfa zanthenda; sadzaliridwa maliro, sadzaikidwa; adzakhala ngati ndowe panthaka; ndipo adzathedwa lupanga, ndi njala; ndipo mitembo yao idzakhala cakudya ca mbalame za kumlengalenga, ndi zirombo za dziko lapansi.
5 Pakuti Yehova atero, Usalowe m'nyumba ya maliro, usanke kukacita maliro ao, kapena kuwalirira; pakuti ndacotsa mtendere wanga pa anthu awa, cifundo ndi nsoni zokoma, ati Yehova.
6 Akuru ndi ang'onong'ono adzafa m'dziko muno; sadzaikidwa, anthu sadzacita maliro ao, sadzadziceka, sadzadziyeseza adazi, cifukwa ca iwo;
7 anthu sadzawagawira mkate pamaliro, kuti atonthoze mitima yao cifukwa ca akufa, anthu sadzapatsa iwo cikho ca kutonthoza kuti acimwe cifukwa ca atate ao kapena mai wao.
8 Usalowe m'nyumba ya madyerero kukhala nao, ndi kudya ndi kumwa.
9 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli; Taonani, ndidzaletsa pano, pamaso panu masiku anu, mau akukondwerera ndi mau akusangalala, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi.
10 Ndipo padzakhala, pamene udzaonetsa anthu awa mau awa onse, ndipo iwo adzati kwa iwe, Cifukwa cace nciani kuti Yehova watinenera ife coipa cacikuru ici? mphulupulu yathu ndi yanji? cimo lathu lanji limene tacimwira Yehova Mulungu wathu?
11 Pamenepo uziti kwa iwo, Cifukwa makolo anu anandisiya Ine, ati Yehova, natsata milungu yina, naitumikira, naigwadira, nandisiya Ine, osasunga cilamulo canga;
12 ndipo mwacita zoipa zopambana makolo anu; pakuti, taonani, muyenda yense potsata kuumirira kwa mtima wace woipa, kuti musandimvere Ine;
13 cifukwa cace ndidzakuturutsani inu m'dziko muno munke ku dziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu yina usana ndi usiku, kumene sindidzacitira inu cifundo.
14 Cifukwa cace, taonani, masiku adza, ati Yehova, kuti sadzanenanso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kuwaturutsa m'dziko la Aigupto.
15 Koma, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kucokera ku dziko la kumpoto, ndi ku maiko ena kumene anawapitikitsirako; ndipo ndidzawabwezanso ku dziko lao limene ndinapatsa makolo ao.
16 Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pace ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.
17 Pakuti maso anga ali pa njira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga,
18 Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi cimo lao cowirikiza; cifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza colowa canga ndi zonyansa zao.
19 Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kucokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira colowa ca bodza lokha, zopanda pace ndi zinthu zosapindula nazo.
20 Kodi munthu adzadzipangira yekha milungu, imene siiri milungu?
21 Cifukwa cace, taonani, ndidzadziwitsa iwo kamodzi aka, ndidzawadziwitsa dzanja langa ndi mphamvu yanga; ndipo adzadziwa kuti dzina langa ndine Yehova.