Yeremiya 13 BL92

Fanizo la mpango wabafuta lifanizira kulangidwa kwao

1 Atero Yehova kwa ine, Pita, udzigulire mpango wabafuta, nudzimangire m'cuuno mwako, usauike m'madzi.

2 Ndipo ndinagula mpango monga mwa mau a Yehova, ndi kubvala m'cuuno mwanga.

3 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yaciwiri, kuti,

4 Tenga mpango umene unaugula, umene uli m'cuuno mwako, nuuke, nupite ku Firate, nuubise m'menemo m'phanga la m'mwala.

5 Ndipo ndinapita, ndinaubisa pa Firate, monga Yehova anandiuza ine.

6 Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati kwa ine, Uka, pita ku Firate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.

7 Ndipo ndinanka ku Firate, ndikumba, nditenga mpango m'malo m'mene ndinaubisamo; ndipo, taonani, mpango unaonongeka, wosayenera kanthu.

8 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,

9 Yehova atero, Momwemo ndidzaononga kudzitama kwa Yuda, ndi kudzitama kwakukuru kwa Yerusalemu.

10 Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu yina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.

11 Pakuti monga mpango uthina m'cuuno ca munthu, comweco ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israyeli ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi cilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva.

12 Cifukwa cace uzinena ndi iwo mau awa: Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo; ndipo adzati kwa iwe, Kodi sitidziwitsa bwino kuti matumba onse adzadzazidwa ndi vinyo?

13 Ndipo udzati kwa iwo, Atero Yehova, Taonani, ndidzadzaza ndi ciledzero onse okhala m'dziko muno, ngakhale mafumu onse amene akhala pa mpando wacifumu wa Davide, ndi ansembe, ndi aneneri, ndi onse okhala m'Yerusalemu.

14 Ndipo ndidzaphwanyanitsa wina ndi wina, atate ndi ana, ati Yehova; sindidzakhala ndi cisoni, sindidzapulumutsa, sindidzakhala ndi cifundo, cakuti ndisawaononge.

15 Tamvani inu, Cherani khutu; musanyade, pakuti Yehova wanena.

16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanakhumudwe pa mapiri acizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Ive asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii.

17 Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri cifukwa ca kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, cifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.

18 Nenani kwa mfumu ndi kwa amace wa mfumu, Dzicepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.

19 Midzi ya ku Mwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda wonse wacotsedwa m'ndende wonsewo, wacotsedwa m'nsinga.

20 Tukulani maso anu, taonani iwo amene acokera kumpoto; ziri kuti zoweta zinapatsidwa kwa iwe, zoweta zako zokoma?

21 Udzanena ciani pamene adzaika abale ako akuru ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala?

22 Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine cifukwa ninji? Cifukwa ca coipa cako cacikuru nsaru zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zithende zako zaphwetekwa.

23 Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lace, kapena nyalugwe maanga ace? pamenepo mungathe inunso kucita zabwino, inu amene muzolowera kucita zoipa,

24 Cifukwa cace ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kucipululu.

25 Ici ndi cagwera cako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; cifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama.

26 Cifukwa cace Ine ndidzaonetsa zotopola mikawo zako, pamaso pako, ndipo manyazi ako adzaoneka.

27 Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi cinyerinyeri ca dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?