1 Ndipo Zedekiya mwana wa Yosiya anakhala mfumu m'malo a Koniya mwana wa Yehoyakimu, amene Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo inamlowetsa mfumu m'dziko la Yuda.
2 Koma ngakhale iye, ngakhale atumiki ace, ngakhale anthu a padziko, sanamvere mau a Yehova, amene ananena mwa Yeremiya mneneri.
3 Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukali mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maseya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu.
4 Ndipo Yeremiya analikuyendayenda mwa anthu; cifukwa asanamuike iye m'nyumba yandende.
5 Ndipo nkhondo ya Farao inaturuka m'Aigupto; ndipo pamene Akasidi omangira misasa Yerusalemu anamva mbiri yao, anacoka ku Yerusalemu.
6 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya mneneri, kuti,
7 Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakuturukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Aigupto ku dziko lao.
8 Ndipo Akasidi adzabweranso, nadzamenyana ndi mudzi uwu; ndipo adzaulanda, nadzautentha ndi moto.
9 Yehova atero: Musadzinyenge, kuti, Akasidi adzaticokera ndithu; pakuti sadzacoka.
10 Pakuti ngakhale mukadakantha nkhondo yonse ya Akasidi akumenyana, nanu, ngakhale akadatsala olasidwa okha okha mwa iwo, koma iwowa akadauka yense m'hema wace ndi kutentha mudzi uwu ndi moto.
11 Ndipo panali pamene nkhondo ya Akasidi inacoka ku Yerusalemu cifukwa ca nkhondo ya Farao,
12 pamenepo Yeremiya anaturuka m'Yerusalemu kumuka ku dziko la Benjamini, kukalandira gawo lace kumeneko.
13 Pokhala iye m'cipinda ca Benjamini, kapitao wa alonda anali kumeneko, dzina lace Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya; ndipo iye anamgwira Yeremiya mneneri, nati, Ulinkupandukira kwa Akasidi.
14 Ndipo anati Yeremiya, Kunama kumeneko; ine sindipandukira kwa Akasidi; koma sanamvera iye; ndipo Iriya anamgwira Yeremiya, nanka naye kwa akuru.
15 Ndipo akuru anakwiyira Yeremiya, nampanda iye, namuika m'nyumba yandende m'nyumba ya Yonatani mlembi; pakuti anaiyesa ndende.
16 Atafika Yeremiya ku nyumba yadzenje, ku tizipinda tace nakhalako Yeremiya masiku ambiri;
17 pamenepo Zedekiya mfumu inatuma, ndi kumtenga iye; ndipo mfumu inamfunsa iye m'tseri m'nyumba mwace, niti, Kodi alipo mau ocokera kwa Yehova? Ndipo Yeremiya, anati, Alipo, Anatinso, Mudzaperekedwa m'dzanja la mfumu ya ku Babulo.
18 Ndipo Yeremiya anati kwa mfumu Zedekiya, Ndacimwira inu ciani, kapena atumiki anu, kapena anthu awa, kuti mwandiika m'nyumba yandende?
19 Tsopano ali kuti aneneri anu, amene ananenera inu, kuti, Mfumu ya ku Babulo sidzakudzerani inu, kapena dziko lino?
20 Tsopano tamvanitu, mbuyanga mfumu; pembedzero langa ligwe pamaso panu; kuti musandibwezere ku nyumba ya Yonatani mlembi, ndingafe kumeneko.
21 Ndipo Zedekiya mfumu analamula, ndipo anamuika Yeremiya m'bwalo la kaidi, tsiku ndi tsiku, nampatsa mkate wofuma ku mseu wa oumba mikate, mpaka unatha mkate wonse wa m'mudzi. Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi.