Yeremiya 28 BL92

Yeremiya atsutsana ndi mneneri wonyenga, Hananiya

1 Ndipo panali caka comweco, poyamba Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda, caka cacinai, mwezi wacisanu, kuti Hananiya mwana wa Azuri mneneri, amene anali wa ku Gibeoni, ananena ndi ine m'nyumba ya Yehova, pamaso pa ansembe ndi pa anthu onse, kuti,

2 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, kuti, Ndatyola gori la mfumu ya ku Babulo.

3 Zisanapite zaka ziwiri zamphumphu Ine ndidzabwezeranso kumalo kuno zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anazicotsa muno, kunka nazo ku Babulo;

4 ndipo ndidzabwezeranso kumalo kuno Yekoniya mwana wace wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi am'nsinga onse a Yuda, amene ananka ku Babulo, ati Yehova: pakuti ndidzatyola gori la mfumu ya ku Babulo.

5 Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa Hananiya mneneri pamaso pa ansembe, ndi pamaso pa anthu onse amene anaima m'nyumba ya Yehova,

6 Yeremiya mneneri anati, Amen: Yehova acite cotero: Yehova atsimikize mau ako amene wanenera, abwezerenso zipangizo za nyumba ya Yehova, ndi onse amene anacotsedwa am'nsinga, kucokera ku Babulo kudza kumalo kuno.

7 Koma mumvetu mau awa amene ndinena m'makutu anu, ndi m'makutu a anthu onse:

8 Aneneri amene analipo kale ndisanakhale ine, nimusanakhale inu, ananenera maiko ambiri, ndi maufumu akuru, za nkhondo, ndi za coipa, ndi za caola.

9 Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzacitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.

10 Pamenepo Hananiya anacotsa gori pa khosi la Yeremiya, nalityola.

11 Ndipo Hananiya ananena pamaso pa anthu onse, kuti, Yehova atero: Comweco ndidzatyola gori la Nebukadinezara mfumu ya Babulo zisanapite zaka ziwiri zamphumphu kulicotsa pa khosi la amitundu onse. Ndipo Yeremiya mneneri anacoka.

12 Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, atatyola Hananiya mneneri gori kulicotsa pa khosi la Yeremiya, kuti,

13 Pita, nunene kwa Hananiya, kuti Yehova atero: Watyola magori amtengo; koma udzapanga m'malo mwao magori acitsulo.

14 Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Ndaika gori lacitsulo pa khosi la amitundu onsewa, kuti amtumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo; ndipo adzamtumikira iye; ndipo ndampatsanso nyama za kuthengo.

15 Ndipo Yeremiya mneneri ananena kwa Hananiya mneneri, Tamvatu, Hananiya; Yehova sanakutuma iwe; koma ukhulupiritsa anthu awa zonama.

16 Cifukwa cace Yehova atero, Taona, Ine ndidzakucotsa iwe kudziko; caka cino udzafa, pakuti wanena zopikisana ndi Yehova.

17 Ndipo anafa Hananiya caka comweco mwezi wacisanu ndi ciwiri.