Yeremiya 27 BL92

Yeremiya awacenjeza agonje kwa mfumu ya ku Babulo

1 Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mau awa anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,

2 Yehova atero kwa ine: Udzipangire zomangira ndi magori, nuziike pakhosi pako;

3 nuzitumize kwa mfumu ya Edomu, ndi kwa mfumu ya Moabu, ndi kwa mfumu ya ana a Amoni, ndi kwa mfumu ya Turo, ndi kwa mfumu ya Zidoni, ndi dzanja la amithenga amene afika ku Yerusalemu kwa Zedekiya mfumu ya Yuda;

4 nuwauze iwo anene kwa ambuyao, kuti, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero: Muzitero kwa ambuyanu:

5 Ine ndinalenga dziko lapansi, anthu ndi nyama zokhala m'dzikomo, ndi mphamvu yanga yaikuru ndi mkono wanga wotambasuka; ndipo ndinapereka ilo kwa iye amene ayenera pamaso panga.

6 Tsopano ndapereka maiko onse awa m'manja a Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga; ndiponso nyama za kuthengo ndampatsa iye kuti zimtumikire.

7 Ndipo amitundu, onse adzamtumikira iye, ndi mwana wace, ndi mdzukulu wace, mpaka yafika nthawi ya dziko lace; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu akuru adzamuyesa iye mtumiki wao.

8 Ndipo padzakhala, kuti mtundu ndi ufumu umene sudzamtumikira Nebukadinezara yemweyo mfumu ya ku Babulo, mtundu umenewo Ine ndidzalanga, ati Yehova, ndi lupanga, ndi njala, ndi caola, mpaka nditatha onse ndi dzanja lace.

9 Koma inu, musamvere aneneri anu, kapena akuombeza anu, kapena maloto anu, kapena alauli anu, kapena obwebweta anu, Musadzatumikira mfumu ya ku Babulo;

10 kakuti iwo akunenerani inu zonama, kuti akucotseni inu m'dziko lanu, kunka kutari kuti ndikupitikitseni inu, ndipo inu mudzathedwa.

11 Koma mtundu umene udzaika khosi lao pansi pa gori la mfumu ya ku Babulo, ndi kumtumikira iye, mtundu umene ndidzaulola ukhalebe m'dziko lao, ati Yehova; ndipo adzalilima, nadzakhala momwemo.

12 Ndipo ndinanena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda monga mau onse amenewa, kuti, Longani makosi anu m'gori la mfumu ya ku Babulo, ndi kumtumikira iye ndi anthu ace, ndipo mudzakhala ndi moyo.

13 Mudzaferanji, iwe ndi anthu anu, ndi lupanga ndi njala, ndi caola, monga wanena Yehova za mtundu umene ukana kumtumikira mfumu ya ku Babulo?

14 Musamvere mau a aneneri amene anena ndi inu, kuti, simudzamtumikira mfumu ya ku Babulo; pakuti akunenerani zonama.

15 Pakuti sindinawatuma iwo, ati Yehova, koma anenera zonama m'dzina langa; kuti ndikupitikitseni inu, kuti mudzathedwe, inu, ndi aneneri amene anenera kwa inu.

16 Ndiponso ndinanena kwa ansembe ndi kwa anthu onsewa, kuti, Yehova atero: Musamvere mau a aneneri anu amene akunenerani inu, kuti, Taonani, zipangizo za nyumba ya Yehova zidzatengedwanso ku Babulo posacedwa; pakuti akunenerani inu zonama.

17 Musamvere amenewa; mtumikireni mfumu ya ku Babulo, ndipo mudzakhala ndi moyo; cifukwa canji mudzi uwu udzakhala bwinja?

18 Koma ngati ndiwo aneneri, ndipo ngati mau a Yehova ali ndi iwo, tsopano apembedzere Yehova wa makamu, kuti zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu, zisanke ku Babulo.

19 Pakuti Yehova wa makamu atero, za zoimiritsa, ndi za thawale, ndi za zoikirapo, ndi za zipangizo zotsala m'mudzi uwu,

20 zimene sanazitenga Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo, pamene anamtenga ndende Yekoniya mwana wace wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, kucokera ku Yerusalemu kunka ku Babulo; ndi akuru onse a Yuda ndi Yerusalemu;

21 inde, atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, za zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu;

22 adzanka nazo ku Babulo, kumeneko zidzakhala, mpaka tsiku limene ndidzayang'anira iwo, ati Yehova; pamenepo ndidzazikweza, ndi kuzibwezera kumalokuno.