Yeremiya 43 BL92

Amtenga Yeremiya napita naye ku Aigupto

1 Ndipo panali pamene Yeremiya anatha kunena kwa anthu onse mau onse a Yehova Mulungu wao, amene anamtuma iye nao Yehova Mulungu wao, mau onse amenewo,

2 pamenepo ananena Azariya mwana wace wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumiza iwe kudzanena, Musalowe m'Aigupto kukhala m'menemo;

3 koma Baruki mwana wace wa Neriya aticicizira inu, mutipereke m'dzanja la Akasidi, kuti atiphe ife, atitengere ife am'nsinga ku Babulo.

4 Ndipo Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, ndi anthu onse sanamvera mau a Yehova, kuti akhale m'dziko la Yuda.

5 Koma Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi akazembe onse: a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera ku mitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m'dziko la Yuda;

6 ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao Wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wace wa Ahikamu, mwana wace wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wace wa Neriya;

7 ndipo anadza nalowa m'dziko la Aigupto; pakuti sanamvera mau a Yehova; ndipo anadza mpaka ku Tapanesi.

Yeremiya aneneratu kuti Nebukadirezara adzagonjetsa Aigupto

8 Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yeremiya m'Tapanesi, kuti,

9 Tenga miyala yaikuru m'dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba ya Farao m'Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda;

10 ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wace wacifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaibvundikira ndi hema wacifumu wace.

11 Ndipo iye adzafika, nadzakantha dziko la Aigupto; nadzapereka kuimfa iwo a kuimfa, ndi kundende iwo a kundende, ndi kulupanga iwo a kulupanga.

12 Ndidzayatsa moto m'nyumba za milungu ya Aigupto; ndipo adzazitentha, nadzaitenga ndende; ndipo adzadzipfunda ndi dziko la Aigupto, monga mbusa abvala cobvala cace; nadzaturuka m'menemo ndi mtendere.

13 Ndipo adzatyola mizati ya zoimiritsa za kacisi wa dzuwa, ali m'dziko la Aigupto; ndi nyumba za milungu ya Aigupto adzazitentha ndi moto.