Yeremiya 8 BL92

1 Nthawi yomweyo, ati Yehova, adzaturutsa m'manda mwao mafupa a mafumu a Yuda, ndi mafupa a akuru ace, ndi mafupa a ansembe, ndi mafupa a aneneri, ndi mafupa a okhala m'Yerusalemu,

2 ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.

3 Ndipo otsala onse amene akutsala pa banja loipa ili adzasankha imfa koposa moyo, ndiwo amene atsala m'malo monse m'mene ndinawaingiramo, ati Yehova wa makamu.

Kulowerera kwa anthu a Mulungu, kulangidwa kudzafikadi

4 Ndiponso udzati kwa iwo, Atero Yehova, Kodi adzagwa, osaukanso? Kodi wina adzacoka, osabweranso?

5 Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu cibwererere? agwiritsa cinyengo, akana kubwera.

6 Ndinachera khutu, ndinamva koma sananena bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zace, ndi kuti, Ndacita ciani? yense anatembenukira njira yace, monga akavalo athamangira m'nkhondo.

7 Inde, cumba ca mlengalenga cidziwa nyengo zace; ndipo njiwa ndi namzeze ndi cingaru ziyang'anira nyengo yakufika kwao; koma anthu anga sadziwa ciweruziro ca Yehova.

8 Bwanji muti, Tiri ndi nzeru ife, ndi malamulo a Yehova ali ndi ife? Koma, taona, peni lonyenga la alembi lacita zonyenga,

9 Anzeru ali ndi manyazi, athedwa nzeru nagwidwa; taonani, akana mau a Yehova; ali nayo nzeru yotani?

10 Cifukwa cace ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse acita zonyenga.

11 Ndipo analipoletsa pang'ono bala la mwana wamkazi wa anthu anga, ndi kuti, Mtendere, mtendere; posakhala mtendere.

12 Kodi anakhala ndi manyazi pamene anacita zonyansa? iai, sanakhala ndi manyazi, sananyala; cifukwa cace adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.

13 Kuwatha ndidzawathetsa iwo, ati Yehova, sipadzakhala mphesa pampesa, kapena nkhuyu pamkuyu, ndipo tsamba lidzafota, ndipo zinthu ndinawapatsa zidzawacokera.

14 Tikhaliranji ife? tasonkhanani, tilowe m'midzi yamalinga, tikhale cete m'menemo; pakuti Yehova Mulungu wathu watikhalitsa ife cete, natipatsa ife madzi a ndulu timwe, pakuti tamcimwira Yehova.

15 Tinayang'anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthawi ya moyo, ndipo taona kuopsedwa!

16 Kumina kwa akavalo ace kunamveka ku Dani; dziko lonse linanthunthumira pa kulira kwa akavalo acewo olimba; cifukwa afika, nadya dziko ndi zonse za momwemo; mudzi ndi amene akhalamo.

17 Pakuti, taonani, ndidzatumiza pa inu njoka, mphiri, zosalola kuitanidwa; ndipo zidzakulumani inu, ati Yehova.

18 Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa cisoni cace! mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.

19 Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ocokera ku dziko lakutari: Kodi m'Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe Mfumu yace? Cifukwa canji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zacabe zacilendo?

20 Masika apita, mphakasa yatha, ndipo ife sitinapulumutsidwe.

21 Bala la mwana wamkazi wa anthu anga ndaphwetekwa nalo; ndada mtima; kudabwa kwandigwira.

22 Kodi mulibe bvunguti m'Gileadi? Kodi mulibe sing'anga m'menemo; analekeranji kucira mwana wamkazi wa anthu anga?