Yeremiya 29 BL92

Kalata wa Yeremiya wolembera kwa Ayuda otengedwa kunka ku Babulo

1 Amenewa ndi mau a kalata uja anatumiza Yeremiya mneneri kucokera ku Yerusalemu kunka kwa akuru otsala a m'nsinga, ndi kwa ansembe, ndi kwa aneneri, ndi kwa anthu onse, amene Nebukadnezara anawatenga ndende ku Yerusalemu kunka ku Babulo;

2 anatero atacoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amace a mfumu ndi adindo ndi akuru a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi acipala,

3 anatumiza kalatayo m'dzanja la Elasa mwana wace wa Safani, ndi Gemariya mwana wace wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatuma ku Babulo kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo, kuti,

4 Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero, kwa am'nsinga onse, amene ndinawatenga ndende ku Yerusalemu kunka nao ku Babulo:

5 Mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zace;

6 tengani akazi, balani ana amuna ndi akazi; kwatitsani ana anu amuna, patsani ananu akazi kwa amuna, kuti abale ana amuna ndi akazi; kuti mubalane pamenepo, musacepe.

7 Nimufune mtendere wa mudzi umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wace inunso mudzakhala ndi mtendere.

8 Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.

9 Pakuti anenera kwa inu zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, ati Yehova.

10 Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babulo, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakucitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.

11 Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a coipa, akukupatsani inu adzukulu ndi ciyembekezero.

12 Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndi kupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu.

13 Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.

14 Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupitikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende.

15 Pakuti mwati, Yehova watiutsira ife aneneri m'Babulo.

16 Pakuti Yehova atero za mfumu imene ikhala pa mpando wacifumu wa Davide, ndi za anthu onse amene akhala m'mudzi uno, abale anu amene sanaturukira pamodzi ndiinu kundende;

17 Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatuma pa iwo lupanga, ndi njala, ndi caola, ndipo ndidzayesa iwo onga nkhuyu zoola, zosadyeka, pokhala nzoipa.

18 Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi caola, ndipo ndidzawapereka akhale oopsyetsa m'maufumu onse a dziko la pansi, akhale citemberero, ndi codabwitsa, ndi cotsonyetsa, ndi citonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapitikitsirako;

19 cifukwa sanamvera mau anga, ati Yehova, amene ndinawatumizira ndi atumiki anga aneneri, ndi kuuka mamawa ndi kuwatuma, koma munakana kumva, ati Yehova.

20 Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m'ndende, amene ndacotsa m'Yerusalemu kunka ku Babulo.

21 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, za Ahabu mwana wace wa Koliya, ndi za Zedekiya mwana wace wa Maseya, amene anenera zonama m'dzina langa: Taonani, Ndidzawapereka m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo; ndipo Iye adzawapha pamaso panu;

22 ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali m'Babulo adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akucitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babulo inaoca m'moto;

23 cifukwa anacita zopusa m'Israyeli, nacita cigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.

24 Ndipo za Semaya Mnehelamu uzinena, kuti,

25 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, kuti, Cifukwa watumiza akalata m'dzina lako iwe mwini kwa anthu onse amene akhala ku Yerusalemu, ndi kwa Zefaniya mwana wace wa Maseya wansembe, ndi kwa ansembe onse, kuti.

26 Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'gori.

27 Ndipo tsopano, walekeranji kumdzudzula Yeremiya wa ku Anatoti, amene amadziyesa mneneri wanu,

28 popeza watitumizira mau ku Babulo, akuti, Undende udzakhalitsa; mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zao?

29 Ndipo Zefaniya wansembe anawerenga kalata amene m'makutu a Yeremiya mneneri.

30 Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, akuti,

31 Uwatumizire mau am'nsinga onse, akuti, Atero Yehova za Semaya Mnehelamu: Cifukwa Semaya wanenera kwa inu, koma Ine sindinamtuma, ndipo anakukhulupiritsani zonama;

32 cifukwa cace atero Yehova, Taonani, ndidzalanga Semaya Mnehelamu, ndi mbeu zace; sadzakhala ndi munthu wakukhala mwa anthu awa, sadzaona za bwino ndidzacitira anthu anga, ati Yehova: cifukwa wanena zopikisana ndi Yehova.