1 Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samueli akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwacotse iwo pamaso panga, aturuke.
2 Ndipo padzakhala, pamene adzati kwa iwe, Titurukire kuti? pamenepo uziti, Atero Yehova: Amene a kuimfa, anke kuimfa; amene a kulupanga, anke kulupanga; amene a kunjala, anke kunjala; ndi amene a kunsinga, anke kunsinga.
3 Ndipo ndidzaika pa iwo mitundu inai, ati Yehova, lupanga lakupha, agaru akung'amba, mbalame za m'mlengalenga, ndi zirombo zapansi, zakulusa ndi kuononga.
4 Ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi, cifukwa ca Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda, cifukwa ca zija anacita m'Yerusalemu.
5 Pakuti ndani adzakucitira iwe cisoni, Yerusalemu? ndani adzakulirira iwe? ndani adzapatukira kudzafunsa za mkhalidwe wako?
6 Iwe wandikana Ine, ati Yehova, wabwerera m'mbuyo; cifukwa cace ndatambasulira dzanja langa pa iwe, ndi kukuononga iwe; ndatopa ndi kulekerera.
7 Ndawakupa ndi mkupo m'zipata za dziko; ndacotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao.
8 Amasiye ao andicurukira Ine kopambana mcenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.
9 Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lace lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova.
10 Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletsa paphindu; koma iwo onse anditemberera.
11 Yehova anati, Ndithu ndidzakulimbitsira iwe zabwino; ndithu ndidzapembedzetsa mdani kwa iwe nthawi ya zoipa ndi nthawi yansautso.
12 Kodi angathe munthu kutyola citsulo, citsulo ca kumpoto, ndi mkuwa?
13 Cuma cako ndi zosungidwa zako ndidzazipereka zifunkhidwe kopanda mtengo wace, icico cidzakugwera cifukwa ca zocimwa zako zonse, m'malire ako onse.
14 Ndipo ndidzawapititsa iwo pamodzi ndi adani ako ku dziko limene sudziwa iwe; pakuti moto wayaka m'mkwiyo wanga, umene udzatentha inu.
15 Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire ine, mundibwezere cilango pa ondisautsa ine; musandicotse m'cipiriro canu; dziwani kuti cifukwa ca Inu ndanyozedwa.
16 Mau anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mau anu anakhala kwa ine cikondwero ndi cisangalalo ca mtima wanga; pakuti ndachedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.
17 Sindinakhala m'msonkhano wa iwo amene asekera-sekera, ndi kusangalala; ndinakhala pandekha cifukwa ca dzanja lanu; pakuti mwandidzaza ndi mkwiyo.
18 Kupweteka kwanga kuti cipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?
19 Cifukwa cace atero Yehova, Ukabwerera pamenepo ndidzakubwezanso, kuti uime pamaso panga; ndipo ukasiyanitsa ca mtengo wace ndi conyansa, udzakhala ngati m'kamwa mwanga; ndipo adzabwerera kwa iwe, koma sudzabwerera kwa iwo.
20 Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipe adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndiri ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova.
21 Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsya.